Yobu 22 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 22:1-30

Mawu a Elifazi

1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,

2“Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu?

Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?

3Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama?

Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?

4“Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula,

kuti azifuna kukukokera ku mlandu?

5Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu?

Kodi machimo ako si opanda malire?

6Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa;

umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.

7Sunawapatse madzi anthu otopa,

ndipo unawamana chakudya anthu anjala,

8ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake,

munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.

9Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu,

ndipo unapondereza ana amasiye.

10Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira,

nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,

11nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu,

nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.

12“Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?

Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!

13Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani?

Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?

14Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona

pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’

15Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale

imene anthu oyipa ankayendamo?

16Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane,

maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.

17Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni!

Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’

18Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,

choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.

19“Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera;

anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.

20Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka

ndipo moto wawononga chuma chawo!’

21“Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere;

ukatero udzaona zabwino.

22Landira malangizo a pakamwa pake

ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.

23Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa;

ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,

24ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi,

golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.

25Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako,

siliva wako wamtengowapatali.

26Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse

ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.

27Udzamupempha ndipo adzakumvera,

ndipo udzapereka zimene unalonjeza.

28Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi,

kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.

29Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’

Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.

30Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa,

ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”