Yobu 19 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 19:1-29

Mawu a Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,

2“Kodi mudzakhala mukundizunza mpaka liti,

ndi kundilasa ndi mawu anuwo?

3Inuyo mwandinyoza kwambiri;

mwanditsutsa mopanda manyazi.

4Ngati ndi zoona kuti ine ndasochera,

cholakwachotu nʼchanga.

5Ngati ndithudi mukudziyika nokha pamwamba panga,

ndi kugwiritsa ntchito kunyozedwa kwanga polimbana nane,

6pamenepa dziwani kuti Mulungu wandilakwira

ndipo wandizinga ukonde wake.

7“Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha;

ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama.

8Mulungu wanditsekera njira yanga kotero sindingathe kudutsa;

waphimba njira zanga ndi mdima.

9Iye wandilanda ulemu wanga

ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga.

10Wandiphwanyaphwanya mbali zonse ndipo ndatheratu;

Iye wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.

11Wandikwiyira ndipo

akundiyesa mmodzi mwa adani ake.

12Ankhondo ake akubwera kwa ine mwamphamvu,

akonzekera zodzalimbana nane

ndipo azungulira nyumba yanga.

13“Mulungu wandisiyanitsa ndi abale anga;

wasandutsa odziwana nane kukhala achilendo kwa ine.

14Abale anga andithawa;

abwenzi anga andiyiwala.

15Anthu odzacheza ku nyumba kwanga ndiponso antchito anga aakazi andisandutsa mlendo;

ndasanduka mlendo mʼmaso mwawo.

16Ndikayitana wa ntchito wanga, iye sandiyankha,

ngakhale ndikapempha ndi pakamwa panga sandichitira kanthu.

17Mpweya wanga umamunyansa mkazi wanga;

ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.

18Inde, ngakhale ana amandinyoza;

akandiona amandinyodola.

19Anzanga onse apamtima amanyansidwa nane;

iwo amene ndinkawakonda andiwukira.

20Ndangotsala khungu ndi mafupa okhaokha;

ndapulumuka lokumbakumba.

21“Mvereni chisoni, inu abwenzi anga, mvereni chisoni,

pakuti dzanja la Mulungu landikantha.

22Chifukwa chiyani mukundilondola ngati Mulungu?

Kodi simunatope nalo thupi langa?

23“Aa, achikhala mawu anga analembedwa,

achikhala analembedwa mʼbuku,

24akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo,

akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa!

25Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo,

ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.

26Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka,

mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.

27Ine ndemwe ndidzamuona Iye

ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi.

Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!

28“Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji,

popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’

29Inu muyenera kuopa lupanga;

pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga;

zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”