Yobu 18 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 18:1-21

Mawu a Bilidadi

1Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

2“Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi?

Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.

3Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe

ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?

4Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako,

kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo?

Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?

5“Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa;

malawi a moto wake sakuwalanso.

6Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima;

nyale ya pambali pake yazima.

7Mayendedwe ake amgugu azilala;

fundo zake zomwe zamugwetsa.

8Mapazi ake amulowetsa mu ukonde

ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.

9Msampha wamkola mwendo;

khwekhwe lamugwiritsitsa.

10Amutchera msampha pansi mobisika;

atchera diwa pa njira yake.

11Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse,

zikutsatira mayendedwe ake onse.

12Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala,

tsoka likumudikira.

13Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse;

miyendo yake, manja ake, zonse zawola.

14Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira,

ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.

15Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo;

awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.

16Mizu yake ikuwuma pansi

ndipo nthambi zake zikufota

17Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi;

sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.

18Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima,

ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.

19Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake,

kulibe wotsala kumene iye ankakhala.

20Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake;

anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.

21Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa;

amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”