Yobu 16 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 16:1-22

Mawu a Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,

2“Ndinamvapo zambiri monga zimenezi;

nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.

3Kodi mawu anu ochulukawo adzatha?

Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?

4Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu,

inuyo mukanakhala monga ndilili inemu;

Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu

ndi kukupukusirani mutu wanga.

5Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani;

chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.

6“Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa;

ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.

7Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu;

mwawononga banja langa lonse.

8Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni;

kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.

9Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane,

amachita kulumira mano;

mdani wanga amandituzulira maso.

10Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza;

amandimenya pa tsaya mwachipongwe

ndipo amagwirizana polimbana nane.

11Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa

ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.

12Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya;

anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya.

Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;

13anthu ake oponya mauta andizungulira.

Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga

ndipo akutayira pansi ndulu yanga.

14Akundivulaza kawirikawiri,

akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.

15“Ndasokerera chiguduli pa thupi langa

ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.

16Maso anga afiira ndi kulira,

ndipo zikope zanga zatupa;

17komatu manja anga sanachite zachiwawa

ndipo pemphero langa ndi lolungama.

18“Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga;

kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!

19Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba;

wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.

20Wondipembedzera ndi bwenzi langa,

pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;

21iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu

monga munthu amadandaulira bwenzi lake.

22“Pakuti sipapita zaka zambiri

ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”