Yobu 15 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 15:1-35

Mawu a Elifazi

1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,

2“Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere,

kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?

3Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake,

kapena kuyankhula mawu opanda phindu?

4Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu

ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.

5Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo;

ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.

6Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga;

milomo yakoyo ikukutsutsa.

7“Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?

Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?

8Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu?

Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?

9Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa?

Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?

10Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu,

anthu amvulazakale kupambana abambo ako.

11Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira,

mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?

12Chifukwa chiyani ukupsa mtima,

ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,

13moti ukupsera mtima Mulungu

ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?

14“Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima

kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?

15Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake,

ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,

16nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota,

amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.

17“Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera;

ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,

18zimene anandiphunzitsa anthu anzeru,

sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.

19(Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa

pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).

20Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake,

munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.

21Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake,

pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.

22Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa;

iyeyo ndi woyenera kuphedwa.

23Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya;

amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.

24Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri;

zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,

25chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu

ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.

26Amapita mwa mwano kukalimbana naye

atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.

27“Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa

ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,

28munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka

ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu,

nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.

29Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa,

ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.

30Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo;

lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake,

ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.

31Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe,

pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.

32Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane,

ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.

33Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse,

adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.

34Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala

ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.

35Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa;

mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”