Yobu 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 12:1-25

Mawu a Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,

2“Ndithudi inuyo ndinu anthu

ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!

3Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu;

ineyo sindine munthu wamba kwa inu.

Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?

4“Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga,

ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha.

Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!

5Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka.

Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.

6Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere,

ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino,

amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.

7“Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa,

kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;

8kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa,

kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.

9Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa

kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?

10Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse,

ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.

11Kodi khutu sindiye limene limamva mawu

monga mmene lilime limalawira chakudya?

12Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba?

Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?

13“Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu;

uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.

14Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso.

Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.

15Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma;

akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.

16Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana;

munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.

17Iye amalanda aphungu nzeru zawo

ndipo amapusitsa oweruza.

18Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo

ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.

19Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo

ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.

20Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika

ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.

21Iye amanyoza anthu otchuka

ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.

22Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima

ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.

23Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso;

amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.

24Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi;

amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.

25Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira;

Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.