Yobu 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 11:1-20

Mawu a Zofari

1Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,

2“Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa?

Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?

3Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku?

Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?

4Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika

ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’

5Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula

kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe

6ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake,

pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri.

Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.

7“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu?

Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?

8Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani?

Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani?

9Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi

ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.

10“Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende

nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?

11Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo;

akaona choyipa, kodi sachizindikira?

12Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru

monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.

13“Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye

ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,

14ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako

ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,

15udzatukula mutu wako wosachita manyazi;

udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.

16Udzayiwala ndithu zowawa zako,

zidzakhala ngati madzi amene apita kale.

17Moyo wako udzawala kupambana usana,

ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.

18Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo;

ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.

19Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza

ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.

20Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza,

ndipo adzasowa njira yothawirapo;

chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”