Yobu 10 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 10:1-22

1“Ine ndatopa nawo moyo wanga;

choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka

ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga.

2Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa,

koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine.

3Kodi mumakondwera mukamandizunza,

kunyoza ntchito ya manja anu,

chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?

4Kodi maso anu ali ngati a munthu?

Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu?

5Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,

kapena zaka zanu ngati zaka za munthu,

6kuti Inu mufufuze zolakwa zanga

ndi kulondola tchimo langa,

7ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa

ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?

8“Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu.

Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?

9Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi,

kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?

10Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale,

suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga?

11Munandikuta ndi khungu ndi mnofu

ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?

12Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu,

ndipo munasamalira bwino moyo wanga.

13“Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu,

ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu:

14Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa

ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga.

15Ngati ndili wolakwa, tsoka langa!

Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga,

pakuti ndagwidwa ndi manyazi

ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga.

16Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango

ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu.

17Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane

ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi

magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira.

18“Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe?

Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.

19Ndikanapanda kubadwa,

kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda!

20Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha?

Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha

21ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako

ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani,

22ku dziko la mdima wandiweyani

ndi chisokonezo,

kumene kuwala kumakhala ngati mdima.”