Yesaya 9 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 9:1-21

Ufumu wa Mesiya

1Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.

2Anthu oyenda mu mdima

awona kuwala kwakukulu;

kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani

kuwunika kwawafikira.

3Inu mwauchulukitsa mtundu wanu

ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo.

Iwo akukondwa pamaso panu,

ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola,

ngatinso mmene anthu amakondwera

pamene akugawana zolanda ku nkhondo.

4Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani,

inu mwathyola goli

limene limawalemera,

ndodo zimene amamenyera mapewa awo,

ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.

5Nsapato iliyonse ya munthu wankhondo,

ndiponso chovala chilichonse chodonthekera magazi

zidzatenthedwa pa moto

ngati nkhuni.

6Chifukwa mwana watibadwira,

mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,

ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.

Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti

Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,

Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.

7Ulamuliro ndi mtendere wake

zidzakhala zopanda malire.

Iye adzalamulira ufumu wake ali pa

mpando waufumu wa Davide,

ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza

mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo

kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya.

Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse

watsimikiza kuchita zimenezi.

Mkwiyo wa Yehova pa Israeli

8Ambuye atumiza mawu otsutsa Yakobo;

ndipo mawuwo agwera pa Israeli.

9Anthu onse okhala mu

Efereimu ndi okhala mu Samariya,

adzadziwa zimenezi.

Iwo amayankhula modzikuza kuti,

10“Ngakhale njerwa zagumuka,

koma ife tidzamanga ndi miyala yosema.

Mitanda ya mkuyu yagwetsedwa,

koma ife tidzayika mitanda ya mkungudza mʼmalo mwake.”

11Koma Yehova wadzutsa adani kuti alimbane nawo

ndipo wawafulumiza adani awo kuti amenyane nawo.

12Asiriya ochokera kummawa ndi Afilisti ochokera kumadzulo ndipo

ayasama pakamwa kuti adye a Israeli.

Komabe, mkwiyo wake sunawachokere,

mkono wake uli chitambasulire.

13Koma anthu sanabwerere kwa amene anawakantha uja,

ngakhale kufunafuna Yehova Wamphamvuzonse.

14Choncho Yehova adzadula mutu wa Israeli pamodzi ndi mchira womwe,

nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe tsiku limodzi;

15mutuwo ndiye akuluakulu ndi olemekezeka,

mchira ndiye aneneri ophunzitsa zabodza.

16Amene amatsogolera anthuwa ndiwo amawasocheretsa,

ndipo otsogoleredwa amatayika.

17Nʼchifukwa chake Ambuye adzakondwera nawo achinyamata,

ngakhale kuwachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye,

pakuti aliyense ndi wosapembedza Mulungu ndiponso ndi wochimwa ndipo

aliyense amayankhula zopusa.

Komabe, mkwiyo wake sunawachokere,

mkono wake uli chitambasulire.

18Ndithu kuyipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto;

moto wake umanyeketsa mkandankhuku ndi minga,

umayatsa nkhalango yowirira,

ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo.

19Dziko lidzatenthedwa ndi ukali wa Yehova Wamphamvuzonse,

dziko lidzatenthedwa

ndipo anthu adzakhala ngati nkhuni zosonkhera moto;

palibe munthu amene adzachitire chifundo mʼbale wake.

20Kudzanja lamanja adzapeza chakudya nʼkudya,

koma adzakhalabe ndi njala;

kudzanja lamanzere adzapeza chakudya nʼkudya,

koma sadzakhuta.

Aliyense azidzadya ana ake omwe.

21Manase adzadya Efereimu ndipo Efereimu adzadya Manase;

onsewa pamodzi adzadya Yuda.

Komabe pa zonsezi, mkwiyo wake sunawachokere,

mkono wake uli chitambasulire.