Yesaya 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 8:1-22

Asiriya, Chida cha Yehova

1Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira. 2Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”

3Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’ 4Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”

5Yehova anayankhulanso ndi Ine;

6“Popeza anthu a dziko ili akana

madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu,

ndipo akukondwerera Rezini

ndi mwana wa Remaliya,

7nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa

madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo;

mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo.

Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse

ndi mʼmagombe ake onse.

8Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira,

adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi.

Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse,

iwe Imanueli!”

9Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere!

Tamverani, inu mayiko onse akutali.

Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!

Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!

10Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu,

kambiranani zochita, koma zidzalephereka,

pakuti Mulungu ali nafe.

Yehova Achenjeza Mneneri

11Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:

12“Usamanene kuti ndi chiwembu,

chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu

usamaope zimene anthuwa amaziopa,

ndipo usamachite nazo mantha.

13Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,

ndiye amene uyenera kumuopa,

ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,

14ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika;

koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala

mwala wopunthwitsa,

mwala umene umapunthwitsa anthu,

thanthwe limene limagwetsa anthu.

Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.

15Anthu ambiri adzapunthwapo

adzagwa ndi kuthyokathyoka,

adzakodwa ndi kugwidwa.”

16Manga umboniwu

ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.

17Ndidzayembekezera Yehova,

amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo.

Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.

18Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.

19Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo, 20kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala. 21Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo. 22Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.