Yesaya 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 7:1-25

Yesaya Achenjeza Ahazi

1Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa.

2Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo.

3Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu. 4Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. 5Mfumu ya Siriya, Efereimu ndi mwana wa Remaliya apangana kuti akuchitire choyipa. Akunena kuti, 6‘Tiyeni tikalimbane ndi Yuda. Tiyeni tiliwononge ndi kuligawa; tiligawane pakati pathu, ndipo tilonge ufumu mwana wa Tabeeli kumeneko.’ 7Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi:

“ ‘Zimenezo sizidzatheka,

sizidzachitika konse,

8pakuti Siriya amadalira Damasiko,

ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi.

Zisanathe zaka 65

Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.

9Dziko la Efereimu limadalira Samariya

ndipo Samariya amadalira mwana wa Remaliya basi.

Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu,

ndithu simudzalimba konse.’ ”

10Yehova anayankhulanso ndi Ahazi, 11“Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”

12Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.”

13Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga? 14Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli. 15Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino. 16Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja. 17Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.”

18Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya. 19Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto. 20Tsiku limenelo Ambuye adzalemba ganyu ometa ochokera kutsidya kwa Mtsinje, ndiye mfumu ya ku Asiriya, kudzameta tsitsi lanu la ku mutu ndi la mʼmiyendo ndi ndevu zomwe. 21Tsiku limenelo adzangosunga ngʼombe yayikazi yayingʼono ndi mbuzi ziwiri. 22Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi. 23Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga. 24Anthu adzapita kumeneko kukachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti mʼdziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga. 25Ndipo mʼmapiri monse mʼmene kale munkalimidwa ndi khasu, simudzapitamo kuopa mkandankhuku ndi minga; malowo adzasanduka odyetserako ngʼombe ndi nkhosa.