Yesaya 66 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 66:1-24

Chiweruzo ndi Chiyembekezo

1Yehova akuti,

“Kumwamba ndi mpando wanga waufumu

ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.

Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire,

ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?

2Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,

motero zonsezi ndi zanga?”

Akutero Yehova.

“Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:

amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,

ndipo amamvera mawu anga.

3Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna

amaphanso munthu,

ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa,

amaphanso galu.

Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya

amaperekanso magazi a nkhumba.

Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso

amapembedzanso fano.

Popeza iwo asankha njira zawozawo,

ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.

4Inenso ndawasankhira chilango chowawa

ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija.

Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha,

pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu.

Anachita zoyipa pamaso panga

ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”

5Imvani mawu a Yehova,

inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake:

“Abale anu amene amakudani,

ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti,

‘Yehova alemekezeke

kuti ife tione chimwemwe chanu!’

Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.

6Imvani mfuwu mu mzinda,

imvani phokoso mʼNyumba ya Mulungu!

Limenelo ndi liwu la Yehova,

kulanga adani ake onse.

7“Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa

wachira kale;

asanayambe kumva ululu,

wabala kale mwana wamwamuna.

8Ndani anamvapo zinthu zoterezi?

Ndani anazionapo zinthu zoterezi?

Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi,

kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi?

Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa

nthawi yomweyo anabereka ana ake.

9Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,

koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova.

“Kodi ndingatseke mimba

pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.

10“Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye,

inu nonse amene mumakonda Yerusalemu,

kondwera nayeni kwambiri,

nonse amene mumamulira.

11Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake

ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri

wa mʼmawere

a chitonthozo chake.”

12Yehova akuti,

“Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje wa madzi,

ndiponso chuma cha anthu a mitundu ina ngati mtsinje wosefukira.

Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene amayi ake amunyamulira pambalipa,

kapena kumufungata pa miyendo yake.

13Monga momwe amayi amasangalatsira mwana wawo,

moteronso Ine ndidzakusangalatsani;

ndipo mudzasangalala chifukwa cha Yerusalemu.”

14Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu.

Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu.

Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira

ndi kuti ndimakwiyira adani anga.

15Taonani, Yehova akubwera ngati moto,

ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu;

Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake

ndi malawi amoto.

16Pakuti Yehova adzalanga anthu onse

ndi moto ndi lupanga,

Yehova adzapha anthu ambiri.

17Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”

18“Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.

19“Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. 20Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo. 21Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.

22“Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova. 23“Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova. 24“Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”