Yesaya 65 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 65:1-25

Chiweruzo ndi Chipulumutso

1“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;

ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.

Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,

ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’

2Tsiku lonse ndatambasulira manja anga

anthu owukira aja,

amene amachita zoyipa,

natsatira zokhumba zawo.

3Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa

mopanda manyazi.

Iwo amapereka nsembe mʼminda

ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.

4Amakatandala ku manda

ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.

Amadya nyama ya nkhumba,

ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.

5Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,

chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’

Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,

ngati moto umene umayaka tsiku lonse.

6“Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;

sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu

chifukwa cha machimo awo

7ndi a makolo awo,”

akutero Yehova.

“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri

ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,

Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata

zimene anachita kale.”

8Yehova akuti,

“Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa

ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,

popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’

Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;

sindidzawononga onse.

9Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,

ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.

Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,

ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.

10Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,

ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe

kwa anthu anga ondifunafuna Ine.

11“Koma inu amene mumasiya Yehova

ndi kuyiwala phiri langa lopatulika,

amene munamukonzera Gadi chakudya

ndi kuthirira Meni chakumwa,

12ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe,

ndipo nonse mudzaphedwa;

chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani,

ndinayankhula koma simunamvere.

Munachita zoyipa pamaso panga

ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”

13Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti,

“Atumiki anga adzadya,

koma inu mudzakhala ndi njala;

atumiki anga adzamwa,

koma inu mudzakhala ndi ludzu;

atumiki anga adzakondwa,

koma inu mudzakhala ndi manyazi.

14Atumiki anga adzayimba

mosangalala,

koma inu mudzalira kwambiri

chifukwa chovutika mu mtima

ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.

15Anthu anga osankhidwa

adzatchula dzina lanu potemberera.

Ambuye Yehova adzakuphani,

koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.

16Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo

adzachita zimenezo kwa Mulungu woona;

ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo

adzalumbira mwa Mulungu woona.

Pakuti mavuto akale adzayiwalika

ndipo adzachotsedwa pamaso panga.

Chilengedwe Chatsopano

17“Taonani, ndikulenga

mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.

Zinthu zakale sizidzakumbukika,

zidzayiwalika kotheratu.

18Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya

chifukwa cha zimene ndikulenga,

pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa

ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.

19Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu

ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.

Kumeneko sikudzamvekanso kulira

ndi mfuwu wodandaula.

20“Ana sadzafa ali akhanda

ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.

Wamngʼono mwa iwo

adzafa ali ndi zaka 100.

Amene adzalephere kufika zaka 100

adzatengedwa kukhala

wotembereredwa.

21Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,

adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.

22Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,

kapena kudzala ndi ena nʼkudya.

Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo

wautali ngati mitengo.

Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito

ya manja awo nthawi yayitali.

23Sadzagwira ntchito pachabe

kapena kubereka ana kuti aone tsoka;

chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,

iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.

24Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.

Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.

25Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.

Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,

koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.

Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala

chinthu chopweteka kapena chowononga,”

akutero Yehova.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以賽亞書 65:1-25

懲罰與拯救

1耶和華說:「我向沒有求問我的人顯現,

讓沒有尋找我的人尋見,

對沒有求告我的國家說,

『我在這裡,我在這裡!』

2我整天伸出雙手招呼一群悖逆的百姓,

他們卻任意妄為,

不走正路,

3不斷地當面惹我發怒。

他們在園中獻祭,

在磚臺上燒香,

4坐在墳場裡,

宿在隱秘處。

他們吃豬肉,

用不潔之物做湯,

5還對人說,『站遠點,

別挨近我,因為我比你聖潔!』

我被這些人氣得鼻孔冒煙,

整天怒火難息。

6看啊,這些都記錄在我面前,

我不會再保持緘默,

我要報應他們,

7按他們和他們祖先的罪報應他們。

我必按他們的所作所為報應他們,

因為他們在山上燒香,

在丘陵上褻瀆我。

這是耶和華說的。」

8耶和華說:「人發現一串葡萄尚可釀造新酒時,

一定會說,『不要毀壞它,

裡面還有好葡萄。』

同樣,因我僕人的緣故,

我也不會把他們全部毀滅。

9「我必使雅各的後裔興起,

使猶大人興起,

繼承我的群山。

我揀選的子民必擁有那片土地,

我的僕人必在那裡安居。

10沙崙必成為牧放羊群的草場,

亞割谷必成為牛群休憩的地方,

這些地方必屬於尋求我的人。

11但至於你們這些背棄我、

忘記我的聖山、

擺宴供奉幸運之神、

調酒祭奠命運之神的人,

12我要使你們註定被殺,

喪身刀下。

因為我呼喚你們,你們不回應;

我講話,你們不聆聽。

你們做我視為惡的事,

專行令我不悅的事。」

13所以主耶和華說:

「看啊,我的僕人必有吃有喝,

你們卻要饑渴交加;

我的僕人必歡喜,

你們卻要受羞辱;

14我的僕人必歡喜快樂,

揚聲歌唱,

你們卻要傷心欲絕,

嚎啕大哭。

15我的選民必用你們的名字作咒詛,

主耶和華必殺死你們,

給祂的僕人另起名字。

16因此,在地上求福祉的人都必向信實的上帝祈求,

在地上起誓的人都必憑信實的上帝起誓。

因為過去的苦難已經被遺忘,

從我眼前消失了。

新天新地

17「看啊,我要創造新天新地,

過去的一切都要被遺忘,

從記憶中消失。

18你們要因我創造的一切而永遠歡喜快樂。

看啊,我要創造一個充滿喜樂的耶路撒冷

其中的居民個個歡欣。

19我必因耶路撒冷而歡喜,

因我的子民而快樂。

城裡再聽不見哭泣和哀號聲。

20再沒有只活幾天便夭折的嬰兒,

也沒有壽數未盡便死的老人,

因為滿了百歲便死的人不過算是青年,

不足百歲便死的人被視為受了咒詛。

21他們要建造房屋,安然居住,

栽種葡萄園,吃園中的果子。

22他們建的房屋再不會被別人居住,

他們種的果實再不會被別人享用。

我的子民必像樹木一樣長壽,

我揀選的人必長享自己親手勞碌的成果。

23他們不會徒勞,

他們的孩子也不會遇到災禍,

因為他們及其子孫是蒙上帝賜福的人。

24他們還沒有求告,

我就已經應允;

他們正要禱告,

我就已經垂聽。

25豺狼和綿羊必一起吃草,

獅子必像牛一樣吃草,

蛇必以塵土為食。

在我的整個聖山上,

牠們都不傷人,不害物。

這是耶和華說的。」