Yesaya 64 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 64:1-12

1Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,

kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!

2Monga momwe moto umatenthera tchire

ndiponso kuwiritsa madzi,

tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,

ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.

3Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,

ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.

4Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo

kapena kuona

Mulungu wina wonga Inu,

amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.

5Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,

amene amakumbukira njira zanu.

Koma Inu munakwiya,

ife tinapitiriza kuchimwa.

Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?

6Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,

ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;

tonse tafota ngati tsamba,

ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.

7Palibe amene amapemphera kwa Inu

kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;

pakuti mwatifulatira

ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.

8Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.

Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;

ife tonse ndi ntchito ya manja anu.

9Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso

musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.

Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,

pakuti tonsefe ndi anthu anu.

10Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;

ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.

11Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,

yatenthedwa ndi moto

ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.

12Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?

Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?