Yesaya 63 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 63:1-19

Yehova Agonjetsa Anthu a Mitundu Ina

1Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu,

atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira?

Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola,

akuyenda mwa mphamvu zake?

“Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo

ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”

2Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,

ngati za munthu wofinya mphesa?

3“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa,

palibe ndi mmodzi yemwe anali nane.

Ndinawapondereza ndili wokwiya

ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali;

magazi awo anadothera pa zovala zanga,

ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.

4Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga;

ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.

5Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza.

Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza;

choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga,

ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.

6Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya;

ndipo ndinawasakaza

ndipo ndinathira magazi awo pansi.”

Matamando ndi Pemphero

7Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,

ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.

Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.

Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake

Yehova wachitira nyumba ya Israeli

zinthu zabwino zambiri.

8Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga,

ana anga amene sadzandinyenga Ine.”

Choncho anawapulumutsa.

9Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,

ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.

Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,

anawanyamula ndikuwatenga

kuyambira kale lomwe.

10Komabe iwo anawukira

ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera.

Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo

ndipo Iye mwini anamenyana nawo.

11Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana,

masiku a Mose mtumiki wake;

ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja,

pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo?

Ali kuti Iye amene anayika

Mzimu Woyera pakati pawo?

12Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa

ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose?

Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona,

kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,

13amene anawayendetsa pa nyanja yozama?

Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu,

iwo sanapunthwe;

14Mzimu Woyera unawapumulitsa

ngati mmene ngʼombe zimapumulira.

Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu

kuti dzina lanu lilemekezeke.”

15Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka,

wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife.

Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti?

Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.

16Koma Inu ndinu Atate athu,

ngakhale Abrahamu satidziwa

kapena Israeli kutivomereza ife;

Inu Yehova, ndinu Atate athu,

kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.

17Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu?

Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso?

Bwererani chifukwa cha atumiki anu;

mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.

18Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa,

adani athu anasakaza malo anu opatulika.

19Ife tili ngati anthu amene

simunawalamulirepo

ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.