Yesaya 62 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 62:1-12

Dzina Latsopano la Ziyoni

1Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,

chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,

mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,

ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.

2Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo

ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.

Adzakuyitanira dzina latsopano

limene adzakupatse ndi Yehova.

3Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,

ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.

4Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”

ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”

Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”

Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”

Chifukwa Yehova akukondwera nawe,

ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.

5Monga mnyamata amakwatira namwali,

momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;

monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,

chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.

6Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda;

sadzakhala chete usana kapena usiku.

Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake

musapumule.

7Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemu

kukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.

8Yehova analumbira atakweza dzanja lake.

Anati,

“Sindidzaperekanso tirigu wako

kuti akhale chakudya cha adani ako,

ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano

pakuti unamuvutikira.

9Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi

ndi kutamanda Yehova,

ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo

mʼmabwalo a Nyumba yanga.”

10Tulukani, dutsani pa zipata!

Konzerani anthu njira.

Lambulani, lambulani msewu waukulu!

Chotsani miyala.

Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.

11Yehova walengeza

ku dziko lonse lapansi kuti,

Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti,

“Taonani, chipulumutso chanu chikubwera;

Yehova akubwera ndi mphotho yake

akubwera nazo zokuyenerani.”

12Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika,

owomboledwa a Yehova;

ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova”

“Mzinda umene Yehova sanawusiye.”

Het Boek

Jesaja 62:1-12

Jeruzalem, de door God gezegende stad

1Omdat ik veel van Sion houd en mijn hart naar Jeruzalem verlangt, zal ik niet ophouden voor haar te bidden, totdat het licht van haar vrijheid daagt en de fakkel van haar redding brandt. 2De volken zullen uw gerechtigheid zien. Koningen zullen worden verblind door uw glorie en God zal u een nieuwe naam geven. 3Hij zal u in zijn hand omhoog houden, een prachtige kroon voor de koning der koningen. 4U zult nooit meer ‘het door God verlaten land’ of ‘het land dat God vergat’ worden genoemd. Uw nieuwe naam zal zijn: ‘het land waar God van houdt’ en ‘de bruid,’ want de Here beleeft vreugde aan u en zal u beschouwen als zijn eigendom. 5Uw kinderen zullen voor u zorgen, o Jeruzalem, met vreugde als van een jonge man die met een jonge vrouw trouwt, en God zal Zich over u verheugen als een bruidegom die in de wolken is met zijn bruid.

6-7 O Jeruzalem, ik heb wachters op uw muren geposteerd die dag en nacht tot God zullen roepen voor de vervulling van zijn beloften. Neem geen rust, u die bidt, en geef God geen rust tot Hij Jeruzalem een hecht fundament geeft en zij over de hele wereld respect en bewondering afdwingt. 8De Here heeft Jeruzalem in al zijn oprechtheid gezworen: ‘Ik zal u nooit meer aan uw vijanden overgeven, vreemde soldaten zullen nooit meer uw koren en wijn weghalen. 9U verbouwde het, u zult het ook eten, God lovend. In de voorhoven van de tempel zult u zelf de wijn drinken die u hebt geperst.’

10Vooruit! Snel! Maak de weg klaar voor de terugkeer van mijn volk! Herstel de wegen, ruim de stenen op en hijs de vlag van Israël. 11Kijk, de Here heeft zijn boodschappers naar elk land gestuurd en zegt: ‘Vertel mijn volk: Ik, de Here, uw God, kom eraan om u te redden en Ik zal u vele geschenken brengen.’ 12En zij zullen ‘het heilige volk’ en ‘de verlosten van de Here’ worden genoemd. Jeruzalem zal ‘begeerde stad’ en ‘door God gezegende stad’ worden genoemd.