Yesaya 57 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 57:1-21

1Anthu olungama amafa,

ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake;

anthu odzipereka amatengedwa,

ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake.

Anthu olungama amatengedwa

kuti tsoka lisawagwere.

2Iwo amene amakhala moyo wolungama

amafa mwamtendere;

amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.

3“Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa,

inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!

4Kodi inu mukuseka yani?

Kodi mukumunena ndani

ndi kupotoza pakamwa panu?

Kodi inu si ana owukira,

zidzukulu za anthu abodza?

5Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu,

ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri.

Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwa

ndiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.

6Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu.

Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo,

ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya.

Kodi zimenezi

zingandichititse kuti ndikukomereni mtima?

7Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali.

Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.

8Mʼnyumba mwanu mwayika

mafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu.

Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu.

Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu,

ndiye mwazilipira kuti mugone nazo.

Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.

9Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafuta

ndi zonunkhira zochuluka.

Munachita kutumiza akazembe anu kutali;

inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko!

10Inu mumatopa ndi maulendo anu,

koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’

Munapezako kumeneko zokhumba zanu

nʼchifukwa chake simunalefuke.

11“Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa,

kotero kuti mwakhala mukundinamiza,

ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe,

kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine?

Kodi mwaleka kundiopa chifukwa choti

ndakhala chete nthawi yayitali?

12Koma ndaonetsa poyera ntchito zanu zomwe mumati nʼzolungama,

ndi mafano anu kuti nʼzosathandiza.

13Pamene mufuwula kupempha thandizo,

mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni!

Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo,

mpweya chabe udzawulutsa mafanowo.

Koma munthu amene amadalira ine

adzalandira dziko lokhalamo.

Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”

Mpumulo kwa Anthu Osweka Mtima

14Ndipo panamveka mawu akuti,

“Undani, undani, konzani msewu!

Chotsani zotchinga pa njira yoyendamo anthu anga.”

15Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse,

amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo,

akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika,

koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima

kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse

ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

16Sindidzawatsutsa anthu mpaka muyaya

kapena kuwapsera mtima nthawi zonse,

popeza kuti ndinalenga anthu anga

ndi kuwapatsa mpweya wamoyo.

17Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera;

ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya,

koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa.

18Ndaona zochita zawo, komabe ndidzawachiritsa;

kuwapumulitsa ndi kuwapatsa mtendere,

19anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo.

Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,”

“Ndipo ndidzawachiritsa.”

Akutero Yehova.

20Koma anthu oyipa ali ngati nyanja yowinduka,

yosatha kukhala bata,

mafunde ake amaponya matope ndi ndere.

21“Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.