Yesaya 54 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 54:1-17

Ulemerero Wamʼtsogolo wa Ziyoni

1“Sangalala, iwe mayi wosabala,

iwe amene sunabalepo mwana;

imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe,

iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;

chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri

kuposa mkazi wokwatiwa,”

akutero Yehova.

2Kulitsa malo omangapo tenti yako,

tambasula kwambiri nsalu zake,

usaleke;

talikitsa zingwe zako,

limbitsa zikhomo zako.

3Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere;

ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina

ndipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa.

4“Usachite mantha; sadzakunyozanso.

Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso.

Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako

ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.

5Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako,

dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu;

dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.

6Yehova wakuyitananso,

uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima,

mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,”

akutero Mulungu wako.

7“Kwa kanthawi kochepa, Ine ndinakusiya,

koma ndidzakutenganso chifukwa ndimakukonda kwambiri.

8Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa

ndili wokwiya kwambiri.

Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya,

ndidzakuchitira chifundo,”

akutero Yehova Mpulumutsi wako.

9“Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa.

Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi.

Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima,

sindidzakudzudzulaninso.

10Ngakhale mapiri atagwedezeka

ndi zitunda kusunthidwa,

koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha.

Pangano langa lamtendere silidzasintha,”

akutero Yehova amene amakuchitira chifundo.

11“Iwe mzinda wozunzika, wokunthidwa ndi namondwe ndiponso wopanda wokutonthoza,

Ine ndidzakongoletsa miyala yako.

Maziko ako ndidzamanga ndi miyala ya safiro.

12Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi.

Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto,

ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali.

13Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,

ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.

14Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni:

Sudzakhalanso wopanikizika,

chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse.

Sudzakhalanso ndi mantha

chifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe.

15Ngati wina adzakuthirani nkhondo, si ndine amene ndachititsa;

aliyense amene adzalimbana nanu adzagonja chifukwa cha iwe.

16“Taona, ndi Ine amene ndinalenga munthu wosula zitsulo

amene amakoleza moto wamakala

ndi kusula zida zoti azigwiritse ntchito.

Ndipo ndine amene ndinalenga munthu wosakaza kuti awononge;

17palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke,

ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa.

Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova.

Chipambano chawo chichokera kwa Ine,”

akutero Yehova.