Yesaya 52 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 52:1-15

1Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni,

vala zilimbe.

Vala zovala zako zokongola,

iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika.

Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa

sadzalowanso pa zipata zako.

2Sasa fumbi lako;

imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu.

Inu omangidwa a ku Ziyoni,

masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.

3Pakuti Yehova akuti,

“Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani,

choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”

4Pakuti Ambuye Yehova akuti,

“Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto;

nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”

5Tsopano Ine Yehova ndikuti,

“Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu,

amene amawalamulira amawanyoza,”

akutero Yehova.

“Ndipo tsiku lonse, akungokhalira

kuchita chipongwe dzina langa.

6Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa;

kotero adzadziwa

kuti ndi Ine amene ndikuyankhula,

Indedi, ndine.”

7Ngokongoladi mapazi a

amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri.

Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere,

chisangalalo ndi chipulumutso.

Iwo akubwera kudzawuza anthu

a ku Ziyoni kuti,

“Mulungu wako ndi mfumu!”

8Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo;

akuyimba pamodzi mwachimwemwe.

Popeza akuona chamaso

kubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.

9Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe,

inu mabwinja a Yerusalemu,

pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,

wapulumutsa Yerusalemu.

10Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika

pamaso pa anthu a mitundu yonse,

ndipo anthu onse a dziko lapansi

adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

11Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko!

Musakhudze kanthu kodetsedwa!

Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova

tulukanimo ndipo mudziyeretse.

12Koma simudzachoka mofulumira

kapena kuchita chothawa;

pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu,

Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.

Kuzunzika ndi Ulemerero wa Mtumiki

13Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake

adzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.

14Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka,

chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu.

Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.

15Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye,

ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye.

Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona,

ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.