Yesaya 5 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 5:1-30

Nyimbo ya Munda Wamphesa

1Ndidzamuyimbira bwenzi langa

nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:

Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa

pa phiri la nthaka yachonde.

2Anatipula nachotsa miyala yonse

ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.

Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo

ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.

Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,

koma ayi, unabala mphesa zosadya.

3“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,

weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.

4Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa

kupambana chomwe ndawuchitira kale?

Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,

bwanji unabala mphesa zosadya?

5Tsopano ndikuwuzani

chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:

ndidzachotsa mpanda wake,

ndipo mundawo udzawonongeka;

ndidzagwetsa khoma lake,

ndipo nyama zidzapondapondamo.

6Ndidzawusandutsa tsala,

udzakhala wosatengulira ndi wosalimira

ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.

Ndidzalamula mitambo

kuti isagwetse mvula pa mundapo.”

7Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse

ndi Aisraeli,

ndipo anthu a ku Yuda ndiwo

minda yake yomukondweretsa.

Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;

mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.

Tsoka ndi Chiweruzo

8Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,

ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda,

mpaka mutalanda malo onse

kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.

9Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti,

“Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja,

nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.

10Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,

kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”

11Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa

nathamangira chakumwa choledzeretsa,

amene amamwa mpaka usiku

kufikira ataledzera kotheratu.

12Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,

matambolini, zitoliro ndi vinyo,

ndipo sasamala ntchito za Yehova,

salemekeza ntchito za manja ake.

13Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo

chifukwa cha kusamvetsa zinthu;

atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala,

ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.

14Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta

ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake;

mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka;

adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.

15Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,

anthu onse adzachepetsedwa,

anthu odzikuza adzachita manyazi.

16Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.

Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.

17Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;

ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.

18Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,

ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,

19amene amanena kuti, “Yehova afulumire,

agwire ntchito yake mwamsanga

kuti ntchitoyo tiyione.

Ntchito zionekere,

zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita,

zichitike kuti tizione.”

20Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino

ndipo zabwino amaziyesa zoyipa,

amene mdima amawuyesa kuwala

ndipo kuwala amakuyesa mdima,

amene zowawasa amaziyesa zotsekemera

ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.

21Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru

ndipo amadziyesa ochenjera.

22Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo

ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,

23amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu

koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.

24Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu

ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,

momwemonso mizu yawo idzawola

ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;

chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,

ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.

25Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;

watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha

Mapiri akugwedezeka,

ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala.

Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke,

dzanja lake likanali chitambasulire;

26Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,

akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.

Awo akubwera,

akubweradi mofulumira kwambiri!

27Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,

palibe amene akusinza kapena kugona;

palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka,

palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.

28Mivi yawo ndi yakuthwa,

mauta awo onse ndi okoka,

ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi,

magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.

29Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,

amabangula ngati misona ya mkango;

imadzuma pamene ikugwira nyama

ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.

30Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula

ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja.

Ndipo wina akakayangʼana dzikolo

adzangoona mdima ndi zovuta;

ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.

New International Version – UK

Isaiah 5:1-30

The song of the vineyard

1I will sing for the one I love

a song about his vineyard:

my loved one had a vineyard

on a fertile hillside.

2He dug it up and cleared it of stones

and planted it with the choicest vines.

He built a watchtower in it

and cut out a winepress as well.

Then he looked for a crop of good grapes,

but it yielded only bad fruit.

3‘Now you dwellers in Jerusalem and people of Judah,

judge between me and my vineyard.

4What more could have been done for my vineyard

than I have done for it?

When I looked for good grapes,

why did it yield only bad?

5Now I will tell you

what I am going to do to my vineyard:

I will take away its hedge,

and it will be destroyed;

I will break down its wall,

and it will be trampled.

6I will make it a wasteland,

neither pruned nor cultivated,

and briers and thorns will grow there.

I will command the clouds

not to rain on it.’

7The vineyard of the Lord Almighty

is the nation of Israel,

and the people of Judah

are the vines he delighted in.

And he looked for justice, but saw bloodshed;

for righteousness, but heard cries of distress.

Woes and judgments

8Woe to you who add house to house

and join field to field

till no space is left

and you live alone in the land.

9The Lord Almighty has declared in my hearing:

‘Surely the great houses will become desolate,

the fine mansions left without occupants.

10A ten-acre vineyard will produce only a bath5:10 That is, about 22 litres of wine;

a homer5:10 That is, probably about 160 kilograms of seed will yield only an ephah5:10 That is, probably about 16 kilograms of grain.’

11Woe to those who rise early in the morning

to run after their drinks,

who stay up late at night

till they are inflamed with wine.

12They have harps and lyres at their banquets,

pipes and tambourines and wine,

but they have no regard for the deeds of the Lord,

no respect for the work of his hands.

13Therefore my people will go into exile

for lack of understanding;

those of high rank will die of hunger

and the common people will be parched with thirst.

14Therefore Death expands its jaws,

opening wide its mouth;

into it will descend their nobles and masses

with all their brawlers and revellers.

15So people will be brought low

and everyone humbled,

the eyes of the arrogant humbled.

16But the Lord Almighty will be exalted by his justice,

and the holy God will be proved holy by his righteous acts.

17Then sheep will graze as in their own pasture;

lambs will feed5:17 Septuagint; Hebrew / strangers will eat among the ruins of the rich.

18Woe to those who draw sin along with cords of deceit,

and wickedness as with cart ropes,

19to those who say, ‘Let God hurry;

let him hasten his work

so that we may see it.

The plan of the Holy One of Israel –

let it approach, let it come into view,

so that we may know it.’

20Woe to those who call evil good

and good evil,

who put darkness for light

and light for darkness,

who put bitter for sweet

and sweet for bitter.

21Woe to those who are wise in their own eyes

and clever in their own sight.

22Woe to those who are heroes at drinking wine

and champions at mixing drinks,

23who acquit the guilty for a bribe,

but deny justice to the innocent.

24Therefore, as tongues of fire lick up straw

and as dry grass sinks down in the flames,

so their roots will decay

and their flowers blow away like dust;

for they have rejected the law of the Lord Almighty

and spurned the word of the Holy One of Israel.

25Therefore the Lord’s anger burns against his people;

his hand is raised and he strikes them down.

The mountains shake,

and the dead bodies are like refuse in the streets.

Yet for all this, his anger is not turned away,

his hand is still upraised.

26He lifts up a banner for the distant nations,

he whistles for those at the ends of the earth.

Here they come,

swiftly and speedily!

27Not one of them grows tired or stumbles,

not one slumbers or sleeps;

not a belt is loosened at the waist,

not a sandal strap is broken.

28Their arrows are sharp,

all their bows are strung;

their horses’ hooves seem like flint,

their chariot wheels like a whirlwind.

29Their roar is like that of the lion,

they roar like young lions;

they growl as they seize their prey

and carry it off with no-one to rescue.

30In that day they will roar over it

like the roaring of the sea.

And if one looks at the land,

there is only darkness and distress;

even the sun will be darkened by clouds.