Yesaya 49 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 49:1-26

Mtumiki wa Yehova

1Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba

tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:

Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,

ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.

2Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,

anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;

Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa

ndipo anandibisa mʼchimake.

3Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.

Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”

4Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito

ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe,

koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,

ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”

5Yehova anandiwumba ine

mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake

kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye

ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,

choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,

ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.

6Yehovayo tsono akuti,

“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,

kuti udzutse mafuko a Yakobo

ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.

Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,

udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”

7Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,

Woyerayo wa Israeli akunena,

amene mitundu ya anthu inamuda,

amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,

“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.

Akalonga nawonso adzagwada pansi.

Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika

ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

8Yehova akuti,

“Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha,

ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza;

ndinakusunga ndi kukusandutsa

kuti ukhale pangano kwa anthu,

kuti dziko libwerere mwakale

ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.

9Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke

ndi a mu mdima kuti aonekere poyera.

“Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira

ndi msipu pa mʼmalo owuma.

10Iwo sadzamva njala kapena ludzu,

kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza;

chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera

ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.

11Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo,

ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.

12Taonani, anthu anga adzachokera kutali,

ena kumpoto, ena kumadzulo,

enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”

13Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga;

kondwera, iwe dziko lapansi;

imbani nyimbo inu mapiri!

Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,

ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.

14Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya,

Ambuye wandiyiwala.”

15“Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere

ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?

Ngakhale iye angathe kuyiwala,

Ine sindidzakuyiwala iwe!

16Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;

makoma ako ndimawaona nthawi zonse.

17Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira,

ndipo amene anakupasula akuchokapo.

18Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane

ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe.

Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo,

anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa

chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’

19“Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa

ndipo dziko lako ndi kusakazidwa,

chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera

ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.

20Ana obadwa nthawi yako yachisoni

adzanena kuti,

‘Malo ano atichepera,

tipatse malo ena woti tikhalemo.’

21Tsono iwe udzadzifunsa kuti,

‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa?

Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena;

ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa.

Ndani anawalera ana amenewa?

Ndinatsala ndekha,

nanga awa, achokera kuti?’ ”

22Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi,

“Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere.

Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere.

Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo

ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.

23Mafumu adzakhala abambo wongokulera

ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera.

Iwo adzagwetsa nkhope

zawo pansi.

Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova;

iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”

24Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo,

kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?

25Koma zimene Yehova akunena ndi izi,

“Ankhondo adzawalanda amʼndende awo,

ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo;

ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu,

ndipo ndidzapulumutsa ana anu.

26Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe;

adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo.

Zikadzatero anthu onse adzadziwa

kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu,

Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”

New International Version

Isaiah 49:1-26

The Servant of the Lord

1Listen to me, you islands;

hear this, you distant nations:

Before I was born the Lord called me;

from my mother’s womb he has spoken my name.

2He made my mouth like a sharpened sword,

in the shadow of his hand he hid me;

he made me into a polished arrow

and concealed me in his quiver.

3He said to me, “You are my servant,

Israel, in whom I will display my splendor.”

4But I said, “I have labored in vain;

I have spent my strength for nothing at all.

Yet what is due me is in the Lord’s hand,

and my reward is with my God.”

5And now the Lord says—

he who formed me in the womb to be his servant

to bring Jacob back to him

and gather Israel to himself,

for I am49:5 Or him, / but Israel would not be gathered; / yet I will be honored in the eyes of the Lord

and my God has been my strength—

6he says:

“It is too small a thing for you to be my servant

to restore the tribes of Jacob

and bring back those of Israel I have kept.

I will also make you a light for the Gentiles,

that my salvation may reach to the ends of the earth.”

7This is what the Lord says—

the Redeemer and Holy One of Israel—

to him who was despised and abhorred by the nation,

to the servant of rulers:

“Kings will see you and stand up,

princes will see and bow down,

because of the Lord, who is faithful,

the Holy One of Israel, who has chosen you.”

Restoration of Israel

8This is what the Lord says:

“In the time of my favor I will answer you,

and in the day of salvation I will help you;

I will keep you and will make you

to be a covenant for the people,

to restore the land

and to reassign its desolate inheritances,

9to say to the captives, ‘Come out,’

and to those in darkness, ‘Be free!’

“They will feed beside the roads

and find pasture on every barren hill.

10They will neither hunger nor thirst,

nor will the desert heat or the sun beat down on them.

He who has compassion on them will guide them

and lead them beside springs of water.

11I will turn all my mountains into roads,

and my highways will be raised up.

12See, they will come from afar—

some from the north, some from the west,

some from the region of Aswan.49:12 Dead Sea Scrolls; Masoretic Text Sinim

13Shout for joy, you heavens;

rejoice, you earth;

burst into song, you mountains!

For the Lord comforts his people

and will have compassion on his afflicted ones.

14But Zion said, “The Lord has forsaken me,

the Lord has forgotten me.”

15“Can a mother forget the baby at her breast

and have no compassion on the child she has borne?

Though she may forget,

I will not forget you!

16See, I have engraved you on the palms of my hands;

your walls are ever before me.

17Your children hasten back,

and those who laid you waste depart from you.

18Lift up your eyes and look around;

all your children gather and come to you.

As surely as I live,” declares the Lord,

“you will wear them all as ornaments;

you will put them on, like a bride.

19“Though you were ruined and made desolate

and your land laid waste,

now you will be too small for your people,

and those who devoured you will be far away.

20The children born during your bereavement

will yet say in your hearing,

‘This place is too small for us;

give us more space to live in.’

21Then you will say in your heart,

‘Who bore me these?

I was bereaved and barren;

I was exiled and rejected.

Who brought these up?

I was left all alone,

but these—where have they come from?’ ”

22This is what the Sovereign Lord says:

“See, I will beckon to the nations,

I will lift up my banner to the peoples;

they will bring your sons in their arms

and carry your daughters on their hips.

23Kings will be your foster fathers,

and their queens your nursing mothers.

They will bow down before you with their faces to the ground;

they will lick the dust at your feet.

Then you will know that I am the Lord;

those who hope in me will not be disappointed.”

24Can plunder be taken from warriors,

or captives be rescued from the fierce49:24 Dead Sea Scrolls, Vulgate and Syriac (see also Septuagint and verse 25); Masoretic Text righteous?

25But this is what the Lord says:

“Yes, captives will be taken from warriors,

and plunder retrieved from the fierce;

I will contend with those who contend with you,

and your children I will save.

26I will make your oppressors eat their own flesh;

they will be drunk on their own blood, as with wine.

Then all mankind will know

that I, the Lord, am your Savior,

your Redeemer, the Mighty One of Jacob.”