Yesaya 48 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 48:1-22

Israeli ndi Nkhutukumve

1“Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo,

inu amene amakutchani dzina lanu Israeli,

ndinu a fuko la Yuda,

inu mumalumbira mʼdzina la Yehova,

ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli,

ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.

2Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika

ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli,

amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:

3Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale,

zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza;

tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.

4Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve

wa nkhongo gwaa,

wa mutu wowuma.

5Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe;

zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe

kuti unganene kuti,

‘Fano langa ndilo lachita zimenezi,

kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’

6Inu munamva zinthu zimenezi.

Kodi inu simungazivomereze?

“Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano

zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.

7Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale;

munali musanazimve mpaka lero lino.

Choncho inu simunganene kuti,

‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’

8Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa;

makutu anu sanali otsekuka.

Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti

chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.

9Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.

Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze.

Sindidzakuwonongani kotheratu.

10Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva;

ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.

11Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi.

Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke?

Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.

Kumasulidwa kwa Israeli

12“Tamvera Ine, iwe Yakobo,

Israeli, amene ndinakuyitana:

Mulungu uja Woyamba

ndi Wotsiriza ndine.

13Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi,

dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga.

Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba

ndi dziko lapansi.

14“Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani:

Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi?

Wokondedwa wa Yehova uja adzachita

zomwe Iye anakonzera Babuloni;

dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.

15Ine, Inetu, ndayankhula;

ndi kumuyitana

ndidzamubweretsa ndine

ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.

16“Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi:

“Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa;

pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.”

Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake

ndi kundituma.

17Yehova, Mpulumutsi wanu,

Woyerayo wa Israeli akuti,

“Ine ndine Yehova Mulungu wanu,

amene ndimakuphunzitsa kuti upindule,

ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.

18Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga,

bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje,

ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.

19Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga,

ana ako akanachuluka ngati fumbi;

dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga

ndipo silikanafafanizidwa konse.”

20Tulukani mʼdziko la Babuloni!

Thawani dziko la Kaldeya!

Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo

ndipo muzilalikire

mpaka kumathero a dziko lapansi;

muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”

21Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu;

anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe;

anangʼamba thanthwelo ndipo

munatuluka madzi.

22“Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.