Yesaya 45 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 45:1-25

1Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake

Koresi amene anamugwira dzanja lamanja

kuti agonjetse mitundu ya anthu

ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,

ndi kutsekula zitseko

kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:

2Ine ndidzayenda patsogolo pako,

ndi kusalaza mapiri;

ndidzaphwanya zitseko za mkuwa

ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.

3Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,

katundu wa pamalo obisika,

kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova

Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.

4Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,

chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,

Ine ndakuyitana pokutchula dzina

ndipo ndakupatsa dzina laulemu

ngakhale iwe sukundidziwa Ine.

5Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;

kupatula Ine palibenso Mulungu wina.

Ndidzakupatsa mphamvu,

ngakhale sukundidziwa Ine,

6kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo

anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.

Ine ndine Yehova,

ndipo palibenso wina.

7Ndimalenga kuwala ndi mdima,

ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;

ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.

8“Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;

mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.

Dziko lapansi litsekuke,

ndipo chipulumutso chiphuke kuti

chilungamo chimereponso;

Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.

9“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,

ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.

Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,

‘Kodi ukuwumba chiyani?’

Kodi ntchito yako inganene kuti,

‘Ulibe luso?’

10Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,

‘Kodi munabereka chiyani?’

Kapena amayi ake kuti,

‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’

11“Yehova

Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,

zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:

Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,

kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?

12Ndine amene ndinapanga dziko lapansi

ndikulenga munthu kuti akhalemo.

Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;

ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.

13Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:

ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.

Iye adzamanganso mzinda wanga

ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,

wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,

akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

14Yehova akuti,

“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.

Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba

adzabwera kwa inu

ndipo adzakhala anthu anu;

iwo adzidzakutsatani pambuyo panu

ali mʼmaunyolo.

Adzakugwadirani

ndi kukupemphani, ponena kuti,

‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;

palibenso mulungu wina.’ ”

15Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika

amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.

16Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.

Adzakhala osokonezeka maganizo.

17Koma Yehova adzapulumutsa Israeli

ndi chipulumutso chamuyaya;

simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka

mpaka kalekale.

18Yehova

analenga zinthu zakumwamba,

Iye ndiye Mulungu;

amene akulenga dziko lapansi,

ndi kulikhazikitsa,

sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,

koma analipanga kuti anthu akhalemo.

Iyeyu akunena kuti:

Ine ndine Yehova,

ndipo palibenso wina.

19Ine sindinayankhule mwachinsinsi,

pamalo ena a mdima;

Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,

“Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”

Ine Yehova, ndimayankhula zoona;

ndikunena zolungama.

20Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;

yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.

Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,

amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.

21Fotokozani mlandu wanu,

mupatsane nzeru nonse pamodzi.

Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?

Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?

Kodi si Ineyo Yehova?

Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,

Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,

palibenso wina kupatula Ine.

22“Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,

inu anthu onse a pa dziko lapansi,

pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.

23Ndalumbira ndekha,

pakamwa panga patulutsa mawu owona,

mawu amene sadzasinthika konse akuti,

bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;

anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.

24Iwo adzanene kwa Ine kuti,

‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”

Onse amene anamuwukira Iye

adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.

25Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli

zidzapambana ndi kupeza ulemerero.