Yesaya 42 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 42:1-25

Mtumiki wa Yehova

1“Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza,

amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye.

Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo,

ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.

2Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu,

kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.

3Bango lophwanyika sadzalithyola,

ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa.

Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;

4sadzafowoka kapena kukhumudwa

mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,

ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”

5Yehova Mulungu

amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,

amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,

amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,

ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,

6“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;

ndikugwira dzanja ndipo

ndidzakuteteza.

Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu

ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.

7Udzatsekula maso a anthu osaona,

udzamasula anthu a mʼndende

ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.

8“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!

Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense

kapena matamando anga kwa mafano.

9Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi,

ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano;

zinthuzo zisanaonekere

Ine ndakudziwitsani.”

Nyimbo Yotamanda Yehova

10Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,

mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi,

inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo.

Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.

11Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo;

midzi ya Akedara ikondwere.

Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe;

afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri.

12Atamande Yehova

ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse.

13Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu,

adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo;

akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo

ndipo adzagonjetsa adani ake.

14Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali,

ndakhala ndili phee osachita kanthu.

Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira,

ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.

15Ndidzawononga mapiri ndi zitunda

ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse;

ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba

ndipo ndidzawumitsa maiwe.

16Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe,

ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo;

ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala

ndipo ndidzasalaza malo osalala.

Zimenezi ndizo ndidzachite;

sindidzawataya.

17Koma onse amene amadalira mafano

amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’

ndidzawachititsa manyazi kotheratu.

Aisraeli Alephera Kuphunzira

18“Imvani, agonthi inu;

yangʼanani osaona inu, kuti muone! 19Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi?

Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma?

Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano,

kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?

20Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale;

makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”

21Chinamukomera Yehova

chifukwa cha chilungamo chake,

kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.

22Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo,

onsewa anawakola mʼmaenje

kapena akuwabisa mʼndende.

Tsono asanduka chofunkha

popanda wina wowapulumutsa

kapena kunena kuti,

“Abwezeni kwawo.”

23Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi

kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo?

24Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha,

ndi Israeli kwa anthu akuba?

Kodi si Yehova,

amene ife tamuchimwirayu?

Pakuti sanathe kutsatira njira zake;

ndipo sanamvere malangizo ake.

25Motero anawakwiyira kwambiri,

nawavutitsa ndi nkhondo.

Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse;

motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.