Yesaya 41 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 41:1-29

Mulungu Thandizo la Israeli

1“Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja!

Alekeni ayandikire ndi kuyankhula;

tiyeni tikhale pamodzi

kuti atiweruze.

2“Ndani anadzutsa wochokera kummawa

uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita?

Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake

ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa

ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi

nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.

3Amawalondola namayenda mosavutika,

mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.

4Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza,

si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu?

Ine Yehova, ndine chiyambi

ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”

5Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa;

anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera.

Akuyandikira pafupi, akubwera;

6aliyense akuthandiza mnzake

ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”

7Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide,

ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo

amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala.

Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.”

Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.

8“Koma Iwe Israeli mtumiki wanga,

Yakobo amene ndakusankha,

Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.

9Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,

ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi.

Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’

Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.

10Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;

usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.

Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,

ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

11“Onse amene akupsera mtima

adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa;

onse amene akukangana nawe

sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.

12Udzafunafuna adani ako,

koma sadzapezeka.

Iwo amene akuchita nawe nkhondo

sadzakhalanso kanthu.

13Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,

amene ndikukugwira dzanja lako lamanja

ndipo ndikuti, usaope;

ndidzakuthandiza.

14Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,

iwe wochepa mphamvu Israeli,

chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”

akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.

15“Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu

chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.

Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,

ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.

16Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso

adzamwazika ndi kamvuluvulu.

Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,

ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:

17“Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,

koma sakuwapeza;

ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.

Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;

Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.

18Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,

ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.

Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi

ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.

19Mʼchipululu ndidzameretsa

mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.

Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo

ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,

20kuti anthu aone ndi kudziwa;

inde, alingalire ndi kumvetsa,

kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;

kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.

21“Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’

Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’

22Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze

zomwe zidzachitike mʼtsogolo.

Tifotokozereni zinthu zamakedzana

tiziganizire

ndi kudziwa zotsatira zake.

Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,

23tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani,

ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu.

Chitani chinthu chabwino kapena choyipa,

ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.

24Koma inu sindinu kanthu

ndipo zochita zanu nʼzopandapake;

amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.

25“Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera,

munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana.

Amapondaponda olamulira ngati matope,

ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.

26Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe,

kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’

Palibe amene ananena,

palibe analengeza zimenezi,

palibe anamva mawu anu.

27Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’

Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.

28Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe,

palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu,

palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.

29Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo!

Zochita zawo si kanthu konse;

mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.