Yesaya 40 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 40:1-31

Mawu a Chitonthozo kwa Anthu a Mulungu

1Atonthozeni, atonthozeni anthu anga,

akutero Mulungu wanu.

2Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu

ndipo muwawuzitse

kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,

tchimo lawo lakhululukidwa.

Ndawalanga mokwanira

chifukwa cha machimo awo onse.

3Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,

“Konzani njira ya Yehova

mʼchipululu;

wongolani njira zake;

msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.

4Chigwa chilichonse achidzaze.

Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse;

Dziko lokumbikakumbika alisalaze,

malo azitundazitunda awasandutse zidikha.

5Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera,

ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona,

pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”

6Wina ananena kuti, “Lengeza.”

Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani?

“Pakuti anthu onse ali ngati udzu

ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.

7Udzu umanyala ndipo maluwa amafota

chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”

Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.

8Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,

koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”

9Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,

kwera pa phiri lalitali.

Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,

fuwula kwambiri,

kweza mawu, usachite mantha;

uza mizinda ya ku Yuda kuti,

“Mulungu wanu akubwera!”

10Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,

ndipo dzanja lake likulamulira,

taonani akubwera ndi mphotho yake

watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.

11Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:

Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake

ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake

ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

12Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,

kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?

Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,

kapena kuyeza kulemera kwa

mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?

13Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova

kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?

14Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,

kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?

Iye anapempha nzeru kwa yani

ndi njira ya kumvetsa zinthu?

15Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.

Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;

mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.

16Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,

ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.

17Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;

Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu

ndi cha chabechabe.

18Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?

Kodi mungamufanizire ndi chiyani?

19Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga

ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide

naliveka mkanda wasiliva.

20Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere

amasankha mtengo umene sudzawola,

nafunafuna mʼmisiri waluso woti

amupangire fano limene silingasunthike.

21Kodi simukudziwa?

Kodi simunamve?

Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?

Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?

22Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,

Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.

Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,

nayikunga ngati tenti yokhalamo.

23Amatsitsa pansi mafumu amphamvu

nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.

24Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene

kapena kufesedwa chapompano,

ndi kungoyamba kuzika mizu kumene

ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa

ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.

25Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?

Kapena kodi alipo wofanana nane?”

26Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.

Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?

Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,

nayitana iliyonse ndi dzina lake.

Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,

palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.

27Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena

ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti,

“Yehova sakudziwa mavuto anga,

Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”

28Kodi simukudziwa?

Kodi simunamve?

Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,

ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.

Iye sadzatopa kapena kufowoka

ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.

29Iye amalimbitsa ofowoka

ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.

30Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,

ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;

31koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.