Yesaya 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 4:1-6

1Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri

adzagwira mwamuna mmodzi,

nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu,

ndi kuvala zovala zathu;

inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu.

Tichotseni manyazi aumbeta!”

Nthambi ya Yehova

2Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli. 3Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu. 4Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto. 5Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova. 6Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.