Yesaya 36 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 36:1-22

Senakeribu Awopseza Yerusalemu

1Chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya ku Yuda, nayilanda. 2Kenaka mfumu ya ku Asiriya inatuma kazembe wake wankhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo kuchokera ku Lakisi kupita kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo anayima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe lakumtunda pa msewu wopita ku malo a munda wa mmisiri wochapa zovala. 3Panali anthu atatu. Woyamba anali Eliyakimu mwana wa Hilikiya komanso ndiye woyangʼanira nyumba ya mfumu. Wachiwiri anali Sebina amene anali mlembi wa bwalo; ndipo wachitatu anali Yowa mwana wa Asafu komanso anali wolemba zochitika. Anthu awa anatuluka kukakumana ndi kazembe wa ankhondo uja.

4Kazembe wa ankhondo anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,

“Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani? 5Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? 6Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira. 7Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’

8“Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! 9Iwe ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo. 10Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.”

11Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa anawuza kazembeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”

12Koma kazembeyo anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”

13Tsono kazembeyo anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! 14Zimene mfumu ikunena ndi izi: Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni! 15Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’

16“Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, 17mpaka mfumuyo itabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanulo, dziko limene lili ndi tirigu ndi vinyo watsopano, dziko loyenda mkaka ndi uchi.

18“Inu musalole kuti Hezekiya akusocheretseni pamene iye akuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi alipo mulungu wa anthu a mtundu wina amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? 19Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? 20Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”

21Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”

22Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu; Sebina mlembi wa bwalo; ndi Yowa, mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza zonse zimene anayankhula kazembe uja.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以赛亚书 36:1-22

亚述王入侵犹大

1希西迦王十四年,亚述西拿基立率兵攻打犹大,攻陷所有的坚城。 2然后,亚述王从拉吉差遣将军率领大军去耶路撒冷希西迦王。大军停在上池的水沟旁、通往漂布场的路上。 3希勒迦的儿子宫廷总管以利亚敬、书记舍伯那亚萨的儿子史官约亚出来见亚述的将军。

4亚述的将军对他们说:“你们去告诉希西迦,伟大的亚述王说,‘你凭什么这样自信呢? 5你所谓的战略和军力不过是空话。你究竟倚靠谁,竟敢背叛我? 6看啊,你所倚靠的埃及不过是一根破裂的芦苇,倚靠它的必被刺破手。倚靠埃及王法老的下场都是这样。’ 7也许你说,‘我们倚靠我们的上帝耶和华。’希西迦不是拆毁了祂的庙宇和祭坛,又吩咐犹大耶路撒冷的人只能在这座祭坛前敬拜吗? 8来,跟我主人亚述王打个赌,你若能找到两千骑士,我就给你两千匹马! 9你们即使依靠埃及的战车和骑兵,又怎能打败我主人的一个最小的将领呢? 10更何况我来攻打、毁灭这地方不正是耶和华的意思吗?耶和华吩咐我攻打、毁灭这地方。”

11以利亚敬舍伯那约亚亚述的将军说:“求你用亚兰语跟仆人们说话,我们都听得懂。求你不要用希伯来语跟我们说话,免得城墙上的人听见。” 12亚述的将军却说:“难道我主派我来只对希西迦和你们说这些话吗?不也是对城墙上的人说吗?他们和你们一样都要吃自己的粪,喝自己的尿。”

13于是,他站着用希伯来语大喊:“你们要听伟大的亚述王的话, 14王说,‘你们不要被希西迦欺骗,他不能救你们。 15不要听希西迦的话去倚靠耶和华,说什么耶和华必拯救你们,这城必不会落在亚述王手中。’ 16不要听希西迦的话。亚述王说,‘你们要跟我讲和,出来归顺我。这样,你们就可以吃自己葡萄树和无花果树的果子,喝自己井里的水。 17以后我会来领你们到一个地方,那里和这里一样有五谷和新酒、饼和葡萄园。 18不要让希西迦欺骗你们,以为耶和华必拯救你们。列国的神明中有哪个曾经从亚述王手中救他的国家呢? 19哈马亚珥拔的神明在哪里呢?西法瓦音的神明在哪里呢?他们从我手中救撒玛利亚了吗? 20这些国家的神明中有哪个曾从我手中救自己的国家呢?难道耶和华能从我手中救耶路撒冷吗?’” 21民众默不作声,一言不发,因为希西迦曾吩咐他们不要答话。 22于是,宫廷总管以利亚敬、书记舍伯那和史官约亚都撕裂衣服,去向希西迦禀告亚述的将军说的话。