Yesaya 35 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 35:1-10

Chimwemwe cha Opulumutsidwa

1Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala;

dziko lowuma lidzakondwa

ndi kuchita maluwa. 2Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka

lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe.

Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni,

maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni.

Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova,

ukulu wa Mulungu wathu.

3Limbitsani manja ofowoka,

limbitsani mawondo agwedegwede;

4nenani kwa a mitima yamantha kuti;

“Limbani mtima, musachite mantha;

Mulungu wanu akubwera,

akubwera kudzalipsira;

ndi kudzabwezera chilango adani anu;

akubwera kudzakupulumutsani.”

5Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso

ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.

6Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala,

ndipo osayankhula adzayimba mokondwera.

Akasupe adzatumphuka mʼchipululu

ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,

7mchenga wotentha udzasanduka dziwe,

nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe.

Pamene panali mbuto ya ankhandwe

padzamera udzu ndi bango.

8Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu;

ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika.

Anthu odetsedwa

sadzayendamo mʼmenemo;

zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.

9Kumeneko sikudzakhala mkango,

ngakhale nyama yolusa sidzafikako;

sidzapezeka konse kumeneko.

Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.

10Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera.

Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba;

kumeneko adzakondwa mpaka muyaya.

Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe,

ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.