Yesaya 34 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 34:1-17

Chiweruzo cha Anthu a Mitundu Yonse

1Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve:

tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse:

Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,

dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!

2Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse;

wapsera mtima magulu awo onse ankhondo.

Iye adzawawononga kotheratu,

nawapereka kuti aphedwe.

3Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja,

mitembo yawo idzawola ndi kununkha;

mapiri adzafiira ndi magazi awo.

4Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka

ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala;

nyenyezi zonse zidzayoyoka

ngati masamba ofota a mphesa,

ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.

5Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba;

taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu,

anthu amene ndawawononga kotheratu.”

6Lupanga la Yehova lakhuta magazi,

lakutidwa ndi mafuta;

magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi,

mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna.

Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira

ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.

7Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati,

ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe.

Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha,

ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.

8Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira

ndi kulanga adani a Ziyoni.

9Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula,

ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule;

dziko lake lidzasanduka phula lamoto!

10Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana;

utsi wake udzafuka kosalekeza.

Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado;

palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.

11Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu;

amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo.

Mulungu adzatambalitsa pa Edomu

chingwe choyezera cha chisokonezo

ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.

12Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko;

akalonga ake onse adzachotsedwa.

13Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa,

khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake.

Ankhandwe azidzadya mʼmenemo;

malo okhalamo akadzidzi.

14Avumbwe adzakumana ndi afisi,

ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana.

Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa

ndi kupeza malo opumulirako.

15Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira,

adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake;

akamtema adzasonkhananso kumeneko,

awiriawiri.

16Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga:

mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa;

sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake.

Pakuti Yehova walamula kuti zitero,

ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.

17Yehova wagawa dziko lawo;

wapatsa chilichonse chigawo chake.

Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya

ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.