Yesaya 33 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 33:1-24

Msautso ndi Thandizo

1Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,

amene sunawonongedwepo!

Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,

iwe amene sunanyengedwepo!

Iwe ukadzaleka kuwononga,

udzawonongedwa,

ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,

ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.

2Inu Yehova, mutikomere mtima ife;

tikulakalaka Inu.

Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,

ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.

3Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;

pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.

4Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.

Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.

5Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse

adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.

6Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,

adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;

kuopa Yehova ngati madalitso.

7Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;

akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.

8Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,

mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.

Mdaniyo ndi wosasunga pangano.

Iye amanyoza mboni.

Palibe kulemekezana.

9Dziko likulira ndipo likunka likutha.

Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.

Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.

Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.

10Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka

ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,

ndipo ndidzakwezedwa.

11Zolingalira zanu nʼzachabechabe

ngati udzu wamanyowa.

Mpweya wamoto udzakupserezani.

12Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;

ndi ngati minga yodulidwa.”

13Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;

inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga

14Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;

anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:

Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?

Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”

15Angathe kuti ndi amene amachita zolungama

ndi kuyankhula zoona,

amene amakana phindu lolipeza monyenga

ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu,

amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo

ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.

16Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,

kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.

Azidzalandira chakudya chake

ndipo madzi sadzamusowa.

17Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola

ndi kuona dziko lotambasukira kutali.

18Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:

“Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?

Ali kuti wokhometsa misonkho uja?

Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”

19Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,

anthu aja achiyankhulo chosadziwika,

chachilendo ndi chosamveka.

20Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;

maso anu adzaona Yerusalemu,

mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,

zikhomo zake sizidzazulidwa,

kapena zingwe zake kuduka.

21Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake

ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.

Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,

sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.

22Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,

Yehova ndiye wotilamulira,

Yehova ndiye mfumu yathu;

ndipo ndiye amene adzatipulumutse.

23Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,

sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,

matanga ake sakutheka kutambasuka.

Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri

ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.

24Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”

ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以赛亚书 33:1-24

主必拯救锡安

1你们这些毁灭别人、自己还未被毁灭的人有祸了!

等你们毁灭完了,就毁灭你们。

你们这些欺诈别人、自己还未被欺诈的人有祸了!

等你们欺诈完了,就欺诈你们。

2耶和华啊,求你施恩给我们,

我们等候你。

求你每天早晨都作我们的力量,

在艰难的时候拯救我们。

3你大喊一声,列邦都奔逃;

你一站起来,列国都溃散。

4他们的战利品必被拿走,

就像谷物被蝗虫吃掉一样;

人们像蝗虫一样扑向他们的战利品。

5耶和华受尊崇,

因为祂住在高天之上,

祂必使锡安充满公平和公义。

6祂必成为你一生的保障,

使你得到丰盛的救恩、智慧和知识。

敬畏耶和华是你最大的宝藏。

7看啊,他们的勇士在街上哀号,

求和的使者悲痛哭泣。

8大路荒凉,行人绝迹。

条约被废,城邑被弃,

人民遭藐视。

9地上一片荒凉,

黎巴嫩的树木枯干,

沙仑好像旷野,

巴珊迦密的树叶凋零。

10耶和华说:

“我现在要施展大能,

我必受尊崇。

11你们所谋的像糠秕,

所行的如碎秸,毫无价值。

你们的气息会像火一样烧灭你们自己。

12列邦必被烧成灰烬,

好像割下的荆棘被火焚烧。”

13远方的人啊,

要听一听我的作为。

近处的人啊,

要承认我的大能。

14锡安的罪人恐惧,

不敬虔的人颤抖。

他们说:“我们谁能住在烈火中呢?

谁能住在永不止息的火焰里呢?”

15秉公行义、说话正直、

憎恶不义之财、不受贿赂、

掩耳不听害人之谋、

闭眼不看邪恶之事的人,

16才可以住在高处。

他们的堡垒是坚固的磐石,

他们必不会绝粮断水。

17你们必目睹君王的荣美,

看到辽阔的土地,

18你们必想起以往可怕的情景,

说:“登记人口的在哪里?

收贡银的在哪里?

数城楼的在哪里?”

19你们再也看不见那些残暴之徒了,

他们的言语奇怪、陌生、

无法听懂。

20你们看锡安——我们守节期的城!

你们必看见耶路撒冷成为安宁之地,

像一个永不挪移的帐篷,

橛子永不拔出,

绳索也不会断。

21在那里,威严的耶和华必与我们同在。

那里必如巨川大河流经之地,

敌人的大小船只都无法穿过。

22因为耶和华是我们的审判官,

是我们的立法者,

是我们的君王,

是我们的拯救者。

23敌人的帆索松开,

桅杆晃动不稳,

风帆无法扬起。

那时,大量的战利品将被瓜分,

甚至瘸子都分得一份。

24耶路撒冷必没有居民说:

“我生病了”,

城中百姓的罪恶必得到赦免。