Yesaya 32 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 32:1-20

Ufumu Wachilungamo

1Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo,

ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.

2Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo

ndi malo obisalirapo namondwe,

adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu,

ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.

3Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,

ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.

4Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa,

ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.

5Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake

ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.

6Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru,

amaganiza kuchita zoyipa:

Iye amachita zoyipira Mulungu,

ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova;

anjala sawapatsa chakudya

ndipo aludzu sawapatsa madzi.

7Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso,

iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa.

Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake

ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.

8Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino,

Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.

Akazi a ku Yerusalemu

9Khalani maso, inu akazi

amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji

ndipo imvani mawu anga.

Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!

10Pakapita chaka ndi masiku pangʼono

inu akazi amatama mudzanjenjemera;

chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika

ndipo zipatso sizidzaoneka.

11Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu;

ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu.

Vulani zovala zanu,

ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.

12Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde,

ndi mphesa yawonongeka.

13Mʼdziko la anthu anga

mwamera minga ndi mkandankhuku.

Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero

ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.

14Nyumba yaufumu idzasiyidwa,

mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu;

malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya.

Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.

15Yehova adzatipatsa mzimu wake,

ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde,

ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.

16Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama

ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.

17Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;

zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.

18Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere,

mʼnyumba zodalirika,

ndi malo osatekeseka a mpumulo.

19Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala

ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,

20inutu mudzakhala odalitsika ndithu.

Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse,

ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以賽亞書 32:1-20

公義的君王

1看啊,必有一位君王以公義治國,

官員們必秉公施政。

2每人都像躲避狂風暴雨的庇護所,

如荒漠中的溪流,

又似乾旱之地遮蔭的大磐石。

3人們的眼睛必不再迷濛,

耳朵必能聽見。

4急躁的人必慎思明辨,

口吃的人必說話清楚流利。

5愚昧人必不再被奉為尊貴之人,

惡棍必不再受尊重。

6因為愚昧人說愚昧話,

心裡邪惡,行事不義,

褻瀆耶和華,

使饑餓的人沒飯吃,

使口渴的人沒水喝。

7惡棍們手段邪惡,

用陰謀詭計和謊言毀滅困苦的人,

即使窮人的訴求有理也是枉然。

8高尚的人計劃高尚的事,

在高尚的事上持之以恆。

9生活安逸的婦女啊,

來聽我的聲音!

無憂無慮的女子啊,

要側耳聽我的言語!

10無憂無慮的女子啊,

再過一年多,

你們必因恐懼而戰抖。

那時,必沒有葡萄可摘,

沒有果子可收。

11生活安逸的婦女啊,戰抖吧!

無憂無慮的女子啊,顫慄吧!

你們要脫下衣服,

腰束麻布,

12為美好的田地和碩果纍纍的葡萄樹捶胸痛哭吧!

13為我百姓那長滿荊棘和蒺藜的土地,

為那曾經充滿歡樂的城邑和家庭哀哭吧!

14王宮必被遺棄,

繁榮的城邑必荒蕪,

山岡和瞭望塔必永遠成為野驢的樂園、羊群的草場。

15等到聖靈從上面澆灌我們的時候,

曠野要變為沃野,

沃野上莊稼茂密如林。

16那時,公平必充滿曠野,

公義必遍佈沃野。

17公義必帶來平安,

公義所結的果子是永遠的和平與安寧。

18我的子民必住在平安之地、

安穩之處、平靜之所。

19但冰雹必掃平森林,蕩平城邑。

20你們這些在河邊撒種、自由地牧放牛驢的人有福了!