Yesaya 31 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 31:1-9

Tsoka kwa Amene Amadalira Igupto

1Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo,

amene amadalira akavalo,

nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo

ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo,

koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli,

kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.

2Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga,

ndipo sasintha chimene wanena.

Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa,

komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.

3Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu;

akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu.

Yehova akangotambasula dzanja lake,

amene amapereka chithandizo adzapunthwa,

amene amalandira chithandizocho adzagwa;

onsewo adzathera limodzi.

4Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi:

“Monga mkango kapena msona wamkango umabangula

ukagwira nyama yake,

ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka

ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo,

momwemonso palibe chingaletse

Yehova Wamphamvuzonse

kubwera kudzatchinjiriza

phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.

5Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,

Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;

ndi kumupulumutsa,

iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”

6Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu. 7Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.

8“Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu.

Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga.

Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo

adzagwira ntchito yathangata.

9Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha,

ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha

kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.”

Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni,

ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.