Yesaya 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 3:1-26

Chiweruzo pa Yerusalemu ndi Yuda

1Taonani tsopano, Ambuye

Yehova Wamphamvuzonse,

ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda

zinthu pamodzi ndi thandizo;

adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,

2anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,

oweruza ndi aneneri,

anthu olosera ndi akuluakulu,

3atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,

aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.

4Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;

ana akhanda ndiwo adzawalamulire.

5Anthu adzazunzana,

munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.

Anthu wamba adzanyoza

akuluakulu.

6Munthu adzagwira mʼbale wake

mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,

“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;

lamulira malo opasuka ano!”

7Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,

“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.

Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;

musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”

8Yerusalemu akudzandira,

Yuda akugwa;

zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,

sakulabadira ulemerero wa Mulungu.

9Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;

amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;

salibisa tchimo lawolo.

Tsoka kwa iwo

odziputira okha mavuto.

10Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,

pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.

11Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!

Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.

12Achinyamata akupondereza anthu anga,

ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.

Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;

akukuchotsani pa njira yanu.

13Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;

wakonzeka kuti aweruze anthu ake.

14Yehova akuwazenga milandu

akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:

“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;

nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.

15Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,

nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”

Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.

16Yehova akunena kuti,

“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,

akuyenda atakweza makosi awo,

akukopa amuna ndi maso awo

akuyenda monyangʼama

akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo

17Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;

Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”

18Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi, 19ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope, 20maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa, 21mphete ndi zipini, 22zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama, 23magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.

24Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,

mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;

mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;

mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;

mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.

25Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,

asilikali ako adzafera ku nkhondo.

26Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;

Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.