Yesaya 29 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 29:1-24

Tsoka kwa Mzinda wa Davide

1Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli,

mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo!

Papite chaka chimodzi kapena ziwiri

ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.

2Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli

ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula,

mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.

3Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo;

ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo

ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.

4Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka,

mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi,

adzamveka ngati a mzukwa.

Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.

5Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti.

Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo.

Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,

6Yehova Wamphamvuzonse adzabwera

ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu,

kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.

7Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli

nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga,

chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto,

gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.

8Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya,

koma podzuka ali nayobe njala;

kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa,

koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa.

Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse

chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.

9Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa.

Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya,

ledzerani, koma osati ndi vinyo,

dzandirani, koma osati ndi mowa.

10Yehova wakugonetsani tulo tofa nato.

Watseka maso anu, inu aneneri;

waphimba mitu yanu, inu alosi.

11Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.” 12Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”

13Ambuye akuti,

“Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,

ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,

koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.

Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.

Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.

14Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira

kuwachitira ntchito zodabwitsa;

nzeru za anthu anzeru zidzatha,

luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”

15Tsoka kwa amene amayesetsa

kubisira Yehova maganizo awo,

amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,

“Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”

16Inu mumazondotsa zinthu

ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.

Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti

“Sunandipange ndi iwe?”

Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,

“Iwe sudziwa chilichonse?”

17Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde,

ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?

18Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku,

ndipo anthu osaona amene

ankakhala mu mdima adzapenya.

19Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova;

ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.

20Koma anthu ankhanza adzazimirira,

oseka anzawo sadzaonekanso,

ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.

21Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa,

kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu

ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.

22Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti,

“Anthu anga sadzachitanso manyazi;

nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.

23Akadzaona ana awo ndi

ntchito ya manja anga pakati pawo,

adzatamanda dzina langa loyera;

adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo,

ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.

24Anthu opusa adzapeza nzeru;

onyinyirika adzalandira malangizo.”