Yesaya 25 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 25:1-12

Nyimbo Yotamanda Yehova

1Yehova ndinu Mulungu wanga;

ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,

pakuti mwachita zodabwitsa

zimene munakonzekeratu kalekale

mokhulupirika kwambiri.

2Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala.

Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja,

linga la anthu achilendo lero si mzindanso

ndipo sidzamangidwanso.

3Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani;

mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.

4Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka,

mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake.

Mwakhala ngati pobisalirapo

pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa.

Pakuti anthu ankhanza

ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,

5ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma.

Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.

Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha,

inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.

6Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera

anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.

Phwando la nyama yonona

ndi vinyo wabwino kwambiri.

7Iye adzachotsa kulira

kumene kwaphimba anthu ngati nsalu.

Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.

8Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya,

Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso

mwa munthu aliyense;

adzachotsa manyazi a anthu ake

pa dziko lonse lapansi,

Yehova wayankhula.

9Tsiku limenelo iwo adzati,

“Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu;

ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa.

Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira;

tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”

10Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake;

ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo,

ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.

11Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo,

ngati mmene amachitira munthu wosambira.

Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo

ngakhale luso la manja awo.

12Iye adzagumula malinga awo ataliatali

ndipo adzawagwetsa

ndi kuwaponya pansi,

pa fumbi penipeni.