Yesaya 24 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 24:1-23

Chilango cha Yehova pa Dziko Lapansi

1Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi

ndi kulisandutsa chipululu;

Iye adzasakaza maonekedwe ake

ndi kumwaza anthu ake onse.

2Aliyense zidzamuchitikira mofanana:

wansembe chimodzimodzi munthu wamba,

antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna,

antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi,

wogula chimodzimodzi wogulitsa,

wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa,

okongola chimodzimodzi okongoza.

3Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu

ndi kusakazikiratu.

Yehova wanena mawu awa.

4Dziko lapansi likulira ndipo likufota,

dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma,

anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.

5Anthu ayipitsa dziko lapansi;

posamvera malangizo ake;

pophwanya mawu ake

ndi pangano lake lamuyaya.

6Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi;

anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo,

iwo asakazika

ndipo atsala ochepa okha.

7Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota;

onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.

8Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha,

phokoso la anthu osangalala latha,

zeze wosangalatsa wati zii.

9Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo;

akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.

10Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka;

nyumba iliyonse yatsekedwa.

11Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo;

chimwemwe chonse chatheratu,

palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.

12Mzinda wasanduka bwinja

zipata zake zagumuka.

13Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi

ndiponso pakati pa mitundu ya anthu.

Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa,

kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.

14Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe;

anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.

15Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova;

ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.

16Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda

“Wolungamayo.”

Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu!

Tsoka kwa ine!

Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo,

inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”

17Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje

ndi msampha zikukudikirani.

18Aliyense wothawa phokoso la zoopsa

adzagwa mʼdzenje;

ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo

adzakodwa ndi msampha.

Zitseko zakumwamba zatsekulidwa,

ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.

19Dziko lapansi lathyokathyoka,

ndipo lagawika pakati,

dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.

20Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera

likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba;

lalemedwa ndi machimo ake.

Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.

21Tsiku limenelo Yehova adzalanga

amphamvu a kumwamba

ndiponso mafumu apansi pano.

22Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi

ngati amʼndende amene ali mʼdzenje.

Adzawatsekera mʼndende

ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.

23Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi;

pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira;

pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,

ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以赛亚书 24:1-23

主必审判世界

1看啊,耶和华必摧毁大地,

使大地荒凉。

祂毁坏地面,驱散万民。

2那时,祭司和百姓,

主人和仆人,

主母和婢女,

买的和卖的,

贷的和借的,

债主和债户都必同遭厄运。

3大地必完全毁坏,一片荒凉。

这是耶和华说的。

4大地必衰残枯干,

世界必衰败荒凉,

世上的权贵也必败落。

5大地被世人玷污,

他们违犯律法,

不守律例,背弃永远的约。

6所以大地必遭受咒诅,

世人必因罪而受惩罚。

他们必被焚烧,

所剩无几。

7葡萄树枯萎,新酒停产,

欢乐的人都发出悲叹。

8欢快的鼓声止息,

悦耳的琴音消失,

宴乐的喧闹不复听闻。

9再没有人对酒高歌,

浓酒变得苦涩。

10毁坏的城一片荒凉,

家家户户大门紧闭,无人能进。

11人们因无酒而在街上喊叫;

一切欢乐变作哀愁,

地上喜乐不复存在。

12城里一片荒凉,

城门一片瓦砾。

13世上万民所剩无几,

像打过的橄榄树,

又如摘过的葡萄树。

14劫后余生的人必高声欢呼,

在西方赞美耶和华的威严。

15因此,要在东方尊崇耶和华,

要在众海岛赞美以色列的上帝耶和华的名。

16我们听见从地极传来歌唱声:

“荣耀归给公义者。”

我说:“我完了!

我完了!我有祸了!

因为诡诈的仍然在行诡诈,

极为猖獗。”

17世人啊!

恐怖、陷阱和网罗要临到你们。

18逃避恐怖的必掉进陷阱,

从陷阱爬上来的必被网罗缠住。

天上的水闸开启,

大地的根基摇动。

19大地断裂、崩溃,剧烈震动。

20大地像醉汉东摇西晃,

又像暴风中的茅屋摇来摆去。

它被沉重的罪恶压垮,

再也无法起来。

21到那日,耶和华必在天上惩罚天上的众权能者,

在地上惩罚地上的君王。

22他们必像囚犯一样被聚在一起,

关在牢里,

日后必受惩罚。

23那时,月亮必羞于露面,

太阳必黯然无光,

因为万军之耶和华必在锡安山,

耶路撒冷掌权,

在祂子民的首领面前彰显荣耀。