Yesaya 22 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 22:1-25

Za Chilango cha Yerusalemu

1Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:

Kodi chachitika nʼchiyani,

kuti nonsenu mukwere pa madenga?

2Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,

iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?

Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,

kapena kufera pa nkhondo.

3Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;

koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.

Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,

ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.

4Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;

ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.

Musayesere kunditonthoza

chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”

5Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione

mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo

mʼChigwa cha Masomphenya.

Malinga agumuka,

komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.

6Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta

ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.

Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.

7Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,

ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;

8zonse zoteteza Yuda zachotsedwa.

Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana

zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;

9inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide

anali ndi malo ambiri ogumuka;

munasunga madzi

mu chidziwe chakumunsi.

10Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu

ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.

11Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime

chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,

koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,

kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.

12Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse

anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;

kumeta mutu wanu mpala

ndi kuvala ziguduli.

13Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;

munapha ngʼombe ndi nkhosa;

munadya nyama ndi kumwa vinyo.

Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa

pakuti mawa tifa!”

14Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.

15Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,

amene amayangʼanira nyumba yaufumu:

16Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo

kuti udzikumbire manda kuno,

kudzikumbira manda pa phiri

ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?

17“Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba

ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.

18Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira

ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.

Kumeneko ndiko ukafere

ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.

Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.

19Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako

ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.

20“Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.

25“Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.