Yesaya 21 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 21:1-17

Za Chilango cha Babuloni

1Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja.

Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,

kuchokera ku chipululu,

dziko lochititsa mantha.

2Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya:

Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga.

Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda!

Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.

3Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,

ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;

ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,

ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.

4Mtima wanga ukugunda,

ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;

chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna

chasanduka chinthu choopsa kwa ine.

5Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,

akuyala mphasa,

akudya komanso kumwa!

Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo,

pakani mafuta zishango zanu!”

6Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi;

“Pita, kayike mlonda

kuti azinena zimene akuziona.

7Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo

ndipo akuyenda awiriawiri,

okwera pa bulu

kapena okwera pa ngamira,

mlondayo akhale tcheru kwambiri.”

8Ndipo mlondayo anafuwula kuti,

“Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;

Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.

9Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta

ali ndi gulu la akavalo.

Mmodzi wa iwo akuti,

‘Babuloni wagwa, wagwa!

Mafano onse a milungu yake

agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”

10Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,

ine ndikukuwuzani zimene ndamva

ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,

Mulungu wa Israeli.

Za Chilango cha Edomu

11Uthenga wonena za Duma:

Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,

“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?

Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”

12Mlonda akuyankha kuti,

“Kukucha, koma kudanso.

Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano;

ndipo ubwerenso udzafunse.”

Za Chilango cha Arabiya

13Uthenga wonena za Arabiya:

Inu anthu amalonda a ku Dedani,

amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,

14perekani madzi kwa anthu aludzu.

Inu anthu a ku Tema

perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.

15Iwo akuthawa malupanga,

lupanga losololedwa,

akuthawa uta wokokakoka

ndiponso nkhondo yoopsa.

16Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu. 17Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.