Yesaya 20 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 20:1-6

Za Chilango cha Igupto ndi Kusi

1Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda, 2nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.

3Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi, 4momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto. 5Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi. 6Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以赛亚书 20:1-6

关于埃及和古实的预言

1亚述撒珥根派元帅攻陷非利士亚实突城那年, 2耶和华吩咐亚摩斯的儿子以赛亚脱去身上的麻衣和脚上的鞋。以赛亚便遵命裸身赤足而行。 3耶和华说:“我仆人以赛亚已经裸身赤足行走三年,作为惩罚埃及古实的标记和预兆。 4亚述王必把埃及古实的老老少少裸身赤足地掳走,使埃及蒙受羞辱。 5那些仰赖古实、仗着埃及夸口的人必惊恐羞愧。 6那时,沿海一带的居民必说,‘看啊!我们投靠他们,指望他们救我们脱离亚述,他们竟落到这个地步!我们怎能逃脱呢?’”