Yesaya 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 2:1-22

Phiri la Yehova

1Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:

2Mʼmasiku otsiriza,

phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa

kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,

lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,

ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.

3Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,

“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,

ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.

Iye adzatiphunzitsa njira zake,

ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”

Malangizo adzachokera ku Ziyoni,

mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.

4Iye adzaweruza pakati pa mayiko,

ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.

Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu

ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.

Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,

kapena kuphunziranso za nkhondo.

5Inu nyumba ya Yakobo, bwerani,

tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.

Tsiku la Yehova

6Inu Yehova mwawakana anthu anu,

nyumba ya Yakobo.

Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa;

amawombeza mawula ngati Afilisti,

ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.

7Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide;

ndipo chuma chawo ndi chosatha.

Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo;

ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.

8Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano;

iwo amapembedza ntchito ya manja awo,

amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.

9Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa

ndi kutsitsidwa.

Inu Yehova musawakhululukire.

10Lowani mʼmatanthwe,

bisalani mʼmaenje,

kuthawa kuopsa kwa Yehova

ndi ulemerero wa ufumu wake!

11Kudzikuza kwa anthu kudzatha,

ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa;

Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.

12Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku

limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama,

ndipo adzagonjetsa

onse amphamvu,

13tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali,

ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,

14tsiku la mapiri onse ataliatali

ndiponso la zitunda zonse zazitali,

15tsiku la nsanja zonse zazitali

ndiponso malinga onse olimba,

16tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi

ndiponso la mabwato onse okongola.

17Kudzikuza kwa munthu kudzatha

ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa,

Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,

18ndipo mafano onse adzatheratu.

19Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe

ndi mʼmaenje a nthaka,

kuthawa mkwiyo wa Yehova,

ndiponso ulemerero wa ufumu wake,

pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.

20Tsiku limenelo anthu adzatayira

mfuko ndi mileme

mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide,

amene anawapanga kuti aziwapembedza.

21Adzathawira mʼmapanga a matanthwe

ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka

kuthawa mkwiyo wa Yehova

ndiponso ulemerero wa ufumu wake,

pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.

22Lekani kudalira munthu,

amene moyo wake sukhalira kutha.

Iye angathandize bwanji wina aliyense?