Yesaya 19 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 19:1-25

Za Kulangidwa kwa Igupto

1Uthenga onena za Igupto:

Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro,

ndipo akupita ku Igupto.

Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake,

ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.

2“Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha;

mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake,

mnansi ndi mnansi wake,

mzinda ndi mzinda unzake,

ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.

3Aigupto adzataya mtima

popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo;

adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,

kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.

4Ndidzawapereka Aigupto

kwa olamulira ankhanza,

ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,”

akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.

5Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa,

ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma.

6Ngalande zake zidzanunkha;

ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma.

Bango ndi dulu zidzafota,

7ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo

ndi ku mathiriro a mtsinjewo.

Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailo

zidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso.

8Asodzi adzabuwula ndi kudandaula,

onse amene amaponya mbedza mu Nailo;

onse amene amaponya makoka mʼmadzi

adzalira.

9Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima,

anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo.

10Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,

ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.

11Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru;

aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa.

Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti,

“Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru,

wophunzira wa mafumu akale?”

12Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti?

Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa

zimene Yehova Wamphamvuzonse

wakonza kuchitira dziko la Igupto.

13Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru,

atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa;

atsogoleri a dziko la Igupto

asocheretsa anthu a dzikolo.

14Yehova wasocheretsa

anthu a ku Igupto.

Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita,

ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.

15Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite,

mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango.

16Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga. 17Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.

18Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.

19Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso. 20Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa. 21Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo. 22Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.

23Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. 24Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi. 25Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Исаия 19:1-25

Пророчество о Египте

1Пророчество о Египте.

Вот Вечный восседает на быстром облаке

и несётся в Египет.

Истуканы Египта пред Ним дрожат,

и сердца египтян трепещут.

2– Я подниму египтян на египтян –

брат будет сражаться с братом,

друг – с другом,

город – с городом,

царство – с царством.

3Египтяне падут духом,

и Я расстрою их замыслы.

Они станут вопрошать идолов и духов мёртвых,

вызывателей умерших и чародеев.

4Я предам египтян во власть жестокого господина,

и безжалостный царь будет править ими, –

возвещает Владыка Вечный, Повелитель Сил.

5Воды Нила иссохнут,

пересохнет русло и станет сушей.

6Каналы начнут испускать зловоние,

потоки Египта обмелеют и пересохнут.

Выгорят и тростник, и камыш,

7и другие растения на берегах Нила.

Всякое засеянное поле у Нила засохнет,

будет развеяно и исчезнет.

8Рыбаки будут стенать,

все забрасывающие в Нил крючки заплачут,

бросающие в воду сети впадут в уныние.

9Обрабатывающие лён придут в отчаяние,

ткачи лучших льняных полотен потеряют надежду19:9 Для выращивания льна нужно обилие воды..

10Делающие одежду будут удручены,

и все работающие за плату падут духом.

11Совсем обезумели правители Цоана;

мудрые советники фараона подают глупые советы.

Как вы скажете фараону:

«Я один из мудрецов,

я потомок древних царей»?

12Где теперь твои мудрецы?

Пусть покажут тебе, пусть откроют,

что Вечный, Повелитель Сил, определил Египту.

13Обезумели правители Цоана,

в заблуждении правители Мемфиса19:13 Букв.: «Нофа».,

главы Египта сбили его с пути.

14Вечный излил на них дух замешательства;

они совращают Египет во всех его делах:

шатается он, как пьяный,

ходящий по собственной блевоте.

15Ни голова, ни хвост, ни ветвь пальмы, ни тростник19:15 Здесь имеются в виду разные социальные группы (см. 9:14-15).

ничего не могут сделать для Египта.

16В тот день египтяне станут как женщины – задрожат они от страха перед поднятой рукой Вечного, Повелителя Сил. 17И земля иудейская наведёт на египтян ужас. Всякий, при ком упомянут об Иудее, испугается из-за того, что определил о них Вечный, Повелитель Сил.

18В тот день пять египетских городов будут говорить на языке исроильтян19:18 Букв.: «ханонеев». и клясться в верности Вечному, Повелителю Сил. Один из них будет назван Городом Солнца19:18 То есть Гелиополь. Или: «Город Разрушения»..

19В тот день жертвенник Вечному будет посередине Египта и памятный знак Вечному – на его границе. 20Это будет знамением и свидетельством о Вечном, Повелителе Сил, в земле Египта. Когда они воззовут к Вечному из-за своих притеснителей, Он пошлёт им Спасителя, Который их защитит и избавит. 21Так Вечный откроется египтянам, и в тот день они познают Вечного. Они станут поклоняться, принося жертвы и хлебные приношения; они станут давать Вечному обеты и исполнять их. 22Вечный поразит Египет, поразит их и исцелит. Они обратятся к Вечному, и Он ответит на их мольбу и исцелит их.

23В тот день будет широкая дорога из Египта в Ассирию. Ассирийцы будут ходить в Египет, а египтяне – в Ассирию, и египтяне с ассирийцами будут поклоняться вместе.

24В тот день Исроил будет третьим, вместе с Египтом и Ассирией, благословением для земли. 25Вечный, Повелитель Сил, благословит их, сказав: «Благословен Египет – Мой народ, и Ассирия – дело Моих рук, и Исроил – Моё наследие».