Yesaya 14 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 14:1-32

1Yehova adzachitira chifundo Yakobo;

adzasankhanso Israeli

ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo.

Alendo adzabwera kudzakhala nawo

ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.

2Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli

ku dziko lawo.

Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja

kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.

Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.

Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.

3Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani, 4mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,

Wopsinja uja watha!

Ukali wake uja watha!

5Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,

Iye waphwanya ndodo ya olamulira.

6Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali

powamenya kosalekeza,

Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali

ndikuwazunza kosalekeza.

7Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;

ndipo akuyimba mokondwa.

8Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni

ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,

“Chigwetsedwere chako pansi,

palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”

9Ku manda kwatekeseka

kuti akulandire ukamabwera;

mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri

a dziko lapansi, yadzutsidwa.

Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu

ayimiritsidwa pa mipando yawo.

10Onse adzayankha;

adzanena kwa iwe kuti,

“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;

Iwe wafanana ndi ife.”

11Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,

pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;

mphutsi zayalana pogona pako

ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.

12Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,

iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!

Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,

Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!

13Mu mtima mwako unkanena kuti,

“Ndidzakwera mpaka kumwamba;

ndidzakhazika mpando wanga waufumu

pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;

ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,

pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.

14Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;

ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”

15Koma watsitsidwa mʼmanda

pansi penipeni pa dzenje.

16Anthu akufa adzakupenyetsetsa

nadzamalingalira za iwe nʼkumati,

“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi

ndi kunjenjemeretsa maufumu,

17munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu,

amene anagwetsa mizinda yake

ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”

18Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu

aliyense mʼmanda akeake.

19Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,

ngati nthambi yowola ndi yonyansa.

Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;

amene anabayidwa ndi lupanga,

anatsikira mʼdzenje lamiyala

ngati mtembo woponderezedwa.

20Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu,

chifukwa unawononga dziko lako

ndi kupha anthu ako.

Zidzukulu za anthu oyipa

sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.

21Konzani malo woti muphere ana ake aamuna

chifukwa cha machimo a makolo awo;

kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi

ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.

22Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.

Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.

Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”

akutero Yehova.

23“Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu

ndiponso dambo lamatope;

ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”

akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Za Kulangidwa kwa Asiriya

24Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti,

“Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho,

ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.

25Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;

ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;

ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,

ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”

26Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,

ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.

27Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?

Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?

Za Kulangidwa kwa Afilisti

28Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:

29Musakondwere inu Afilisti nonse

kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;

chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,

ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.

30Osaukitsitsa adzapeza chakudya

ndipo amphawi adzakhala mwamtendere.

Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,

ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.

31Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!

Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!

Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,

ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.

32Kodi tidzawayankha chiyani

amithenga a ku Filisitiya?

“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,

ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”

New International Version

Isaiah 14:1-32

1The Lord will have compassion on Jacob;

once again he will choose Israel

and will settle them in their own land.

Foreigners will join them

and unite with the descendants of Jacob.

2Nations will take them

and bring them to their own place.

And Israel will take possession of the nations

and make them male and female servants in the Lord’s land.

They will make captives of their captors

and rule over their oppressors.

3On the day the Lord gives you relief from your suffering and turmoil and from the harsh labor forced on you, 4you will take up this taunt against the king of Babylon:

How the oppressor has come to an end!

How his fury14:4 Dead Sea Scrolls, Septuagint and Syriac; the meaning of the word in the Masoretic Text is uncertain. has ended!

5The Lord has broken the rod of the wicked,

the scepter of the rulers,

6which in anger struck down peoples

with unceasing blows,

and in fury subdued nations

with relentless aggression.

7All the lands are at rest and at peace;

they break into singing.

8Even the junipers and the cedars of Lebanon

gloat over you and say,

“Now that you have been laid low,

no one comes to cut us down.”

9The realm of the dead below is all astir

to meet you at your coming;

it rouses the spirits of the departed to greet you—

all those who were leaders in the world;

it makes them rise from their thrones—

all those who were kings over the nations.

10They will all respond,

they will say to you,

“You also have become weak, as we are;

you have become like us.”

11All your pomp has been brought down to the grave,

along with the noise of your harps;

maggots are spread out beneath you

and worms cover you.

12How you have fallen from heaven,

morning star, son of the dawn!

You have been cast down to the earth,

you who once laid low the nations!

13You said in your heart,

“I will ascend to the heavens;

I will raise my throne

above the stars of God;

I will sit enthroned on the mount of assembly,

on the utmost heights of Mount Zaphon.14:13 Or of the north; Zaphon was the most sacred mountain of the Canaanites.

14I will ascend above the tops of the clouds;

I will make myself like the Most High.”

15But you are brought down to the realm of the dead,

to the depths of the pit.

16Those who see you stare at you,

they ponder your fate:

“Is this the man who shook the earth

and made kingdoms tremble,

17the man who made the world a wilderness,

who overthrew its cities

and would not let his captives go home?”

18All the kings of the nations lie in state,

each in his own tomb.

19But you are cast out of your tomb

like a rejected branch;

you are covered with the slain,

with those pierced by the sword,

those who descend to the stones of the pit.

Like a corpse trampled underfoot,

20you will not join them in burial,

for you have destroyed your land

and killed your people.

Let the offspring of the wicked

never be mentioned again.

21Prepare a place to slaughter his children

for the sins of their ancestors;

they are not to rise to inherit the land

and cover the earth with their cities.

22“I will rise up against them,”

declares the Lord Almighty.

“I will wipe out Babylon’s name and survivors,

her offspring and descendants,”

declares the Lord.

23“I will turn her into a place for owls

and into swampland;

I will sweep her with the broom of destruction,”

declares the Lord Almighty.

24The Lord Almighty has sworn,

“Surely, as I have planned, so it will be,

and as I have purposed, so it will happen.

25I will crush the Assyrian in my land;

on my mountains I will trample him down.

His yoke will be taken from my people,

and his burden removed from their shoulders.”

26This is the plan determined for the whole world;

this is the hand stretched out over all nations.

27For the Lord Almighty has purposed, and who can thwart him?

His hand is stretched out, and who can turn it back?

A Prophecy Against the Philistines

28This prophecy came in the year King Ahaz died:

29Do not rejoice, all you Philistines,

that the rod that struck you is broken;

from the root of that snake will spring up a viper,

its fruit will be a darting, venomous serpent.

30The poorest of the poor will find pasture,

and the needy will lie down in safety.

But your root I will destroy by famine;

it will slay your survivors.

31Wail, you gate! Howl, you city!

Melt away, all you Philistines!

A cloud of smoke comes from the north,

and there is not a straggler in its ranks.

32What answer shall be given

to the envoys of that nation?

“The Lord has established Zion,

and in her his afflicted people will find refuge.”