Yesaya 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 13:1-22

Kulangidwa Kwa Babuloni

1Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:

2Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see,

muwafuwulire ankhondo;

muwakodole kuti adzalowe pa zipata

za anthu olemekezeka.

3Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga;

ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira

amene amadzikuza ndi chipambano changa.

4Tamvani phokoso ku mapiri,

likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu!

Tamvani phokoso pakati pa maufumu,

ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi!

Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera

kuchita nkhondo.

5Iwo akuchokera ku mayiko akutali,

kuchokera kumalekezero a dziko

Yehova ali ndi zida zake za nkhondo

kuti adzawononge dziko la Babuloni.

6Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira;

lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.

7Zimenezi zinafowoketsa manja onse,

mtima wa munthu aliyense udzachokamo.

8Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu,

zowawa ndi masautso zidzawagwera;

adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka.

Adzayangʼanana mwamantha,

nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.

9Taonani, tsiku la Yehova likubwera,

tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;

kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu

ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.

10Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga

sizidzaonetsa kuwala kwawo.

Dzuwa lidzada potuluka,

ndipo mwezi sudzawala konse.

11Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake,

anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.

Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza,

ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.

12Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino.

Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.

13Tsono ndidzagwedeza miyamba

ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.

Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse

pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.

14Ngati mbawala zosakidwa,

ngati nkhosa zopanda wozikusa,

munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo,

aliyense adzathawira ku dziko lake.

15Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa

adzaphedwa momubaya ndi lupanga.

16Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona;

nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.

17Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva

ndipo sasangalatsidwa ndi golide,

kuti amenyane ndi Ababuloni.

18Adzapha anyamata ndi mauta awo;

sadzachitira chifundo ana

ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.

19Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse.

Anthu ake amawunyadira.

Koma Yehova adzawuwononga

ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.

20Anthu sadzakhalamonso

kapena kukhazikikamo pa mibado yonse;

palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake,

palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.

21Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko,

nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe;

mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi,

ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.

22Mu nsanja zake muzidzalira afisi,

mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe.

Nthawi yake yayandikira

ndipo masiku ake ali pafupi kutha.