Yesaya 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 11:1-16

Za Ufumu Wamtendere wa Mesiya

1Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese

ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.

2Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye

Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu,

Mzimu wauphungu ndi wamphamvu,

Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.

3Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.

Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso,

kapena kugamula mlandu potsata zakumva;

4koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo,

adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi.

Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake;

atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.

5Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake

ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.

6Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa,

kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi,

mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi

ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.

7Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi,

ana awo adzagona pamodzi,

ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.

8Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,

ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.

9Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga

pa phiri lopatulika la Yehova,

pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova

monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.

10Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero. 11Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.

12Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,

ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli;

Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda

kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.

13Nsanje ya Efereimu idzatha,

ndipo adani a Yuda adzatha;

Efereimu sadzachitira nsanje Yuda,

ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.

14Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo;

ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa.

Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu,

ndipo Aamoni adzawagonjera.

15Yehova adzaphwetsa

mwendo wa nyanja ya Igupto;

adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha

pa mtsinje wa Yufurate.

Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri

kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.

16Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira

amene anatsalira ku Asiriya,

monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli

pamene amachokera ku Igupto.