Yesaya 10 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 10:1-34

1Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo,

kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,

2kuwalanda anthu osauka ufulu wawo

ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga,

amalanda zinthu za akazi amasiye

ndi kubera ana amasiye.

3Kodi mudzatani pa tsiku la chilango,

pofika chiwonongeko chochokera kutali?

Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni?

Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?

4Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa

kapena kufa pamodzi ndi ophedwa.

Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere,

mkono wake uli chitambasulire.

Chiweruzo cha Mulungu pa Asiriya

5“Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga,

iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!

6Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu,

ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine,

kukafunkha ndi kulanda chuma,

ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.

7Koma izi si zimene akufuna kukachita,

izi si zimene zili mʼmaganizo mwake;

cholinga chake ndi kukawononga,

kukapulula mitundu yambiri ya anthu.

8Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’

9‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi?

Kodi Hamati sali ngati Aripadi,

nanga Samariya sali ngati Damasiko?

10Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano,

mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;

11nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake

monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’ ”

12Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake. 13Pakuti mfumuyo ikuti,

“ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa,

ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu.

Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu,

ndinafunkha chuma chawo;

ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.

14Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu

ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame,

ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa,

motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse;

palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake,

kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”

15Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito,

kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito?

Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula,

kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!

16Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse

adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu;

kunyada kwa mfumuyo kudzapsa

ndi moto wosazima.

17Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto,

Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto.

Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza

ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.

18Ankhondo ake adzawonongedwa

ngati nkhalango yayikulu

ndi ngati nthaka yachonde.

19Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri,

yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.

Aisraeli Otsala

20Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli,

opulumuka a nyumba ya Yakobo,

sadzadaliranso anthu

amene anawakantha,

koma adzadalira Yehova,

Woyerayo wa Israeli.

21Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo

adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.

22Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja,

otsala okha ndiwo adzabwerere.

Chiwonongeko chalamulidwa,

chidzaonetsa chilungamo chosefukira.

23Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse

monga momwe analamulira.

24Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti,

“Inu anthu anga okhala mu Ziyoni,

musawaope Asiriya,

amene amakukanthani ndi ndodo

nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.

25Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu

ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”

26Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu,

monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu;

ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi

ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.

27Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu,

goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu;

golilo lidzathyoka

chifukwa cha kunenepa kwambiri.

28Adani alowa mu Ayati

apyola ku Migironi;

asunga katundu wawo ku Mikimasi.

29Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti,

“Tikagona ku Geba”

Rama akunjenjemera;

Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.

30Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu!

Tchera khutu, iwe Laisa!

Iwe Anatoti wosauka!

31Anthu a ku Madimena akuthawa;

anthu a ku Gebimu bisalani.

32Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu;

adzagwedeza mikono yawo,

kuopseza anthu a ku Ziyoni,

pa phiri la Yerusalemu.

33Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,

adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo,

mitengo yodzikweza idzadulidwa,

mitengo yayitali idzagwetsedwa.

34Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira;

Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.