Yeremiya 9 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 9:1-26

1Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi,

ndi maso anga ngati kasupe wa misozi!

Ndikanalira usana ndi usiku

kulirira anthu anga amene aphedwa.

2Ndani adzandipatsa malo

ogona mʼchipululu

kuti ndiwasiye anthu anga

ndi kuwachokera kupita kutali;

pakuti onse ndi achigololo,

ndiponso gulu la anthu onyenga.

3“Amapinda lilime lawo ngati uta.

Mʼdzikomo mwadzaza

ndi mabodza okhaokha

osati zoonadi.

Amapitirirabe kuchita zoyipa;

ndipo sandidziwa Ine.”

Akutero Yehova.

4“Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;

asadalire ngakhale abale ake.

Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.

Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.

5Aliyense amamunamiza mʼbale wake

ndipo palibe amene amayankhula choonadi.

Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza;

amalimbika kuchita machimo.

6Iwe wakhalira mʼchinyengo

ndipo ukukana kundidziwa Ine,”

akutero Yehova.

7Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.

Kodi ndingachite nawonso

bwanji chifukwa cha machimo awo?

8Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;

limayankhula zachinyengo.

Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,

koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.

9Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?

akutero Yehova.

‘Kodi ndisawulipsire

mtundu wotere wa anthu?’ ”

10Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri

ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.

Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,

ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.

Mbalame zamlengalenga zathawa

ndipo nyama zakuthengo zachokako.

11Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja,

malo okhalamo ankhandwe;

ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda

kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”

12Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”

13Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala. 14Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.” 15Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu. 16Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”

17Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere;

itanani akazi odziwa kulira bwino.”

18Anthu akuti, “Abwere mofulumira

kuti adzatilire

mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi

ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.

19Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti,

‘Aa! Ife tawonongeka!

Tachita manyazi kwambiri!

Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu

chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”

20Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;

tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.

Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;

aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.

21Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu

ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa;

yapha ana athu mʼmisewu,

ndi achinyamata athu mʼmabwalo.

22Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti,

“ ‘Mitembo ya anthu

idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda,

ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola,

popanda munthu woyitola.’ ”

23Yehova akuti,

“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,

kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake,

kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,

24koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:

kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,

kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,

chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.

Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”

akutero Yehova.

25“Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe. 26Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”