Yeremiya 46 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 46:1-28

1Yehova anamupatsa Yeremiya uthenga wonena za anthu a mitundu ina.

Uthenga Wonena za Igupto

2Kunena za Igupto:

Yehova ananena za gulu lankhondo la Farao Neko mfumu ya ku Igupto limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni analigonjetsa ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda,

3anati, “Konzani zishango zanu ndi malihawo,

ndipo yambanipo kupita ku nkhondo!

4Mangani akavalo,

ndipo kwerani inu okwerapo!

Khalani pa mzere

mutavala zipewa!

Nolani mikondo yanu,

valani malaya anu ankhondo!

5Yeremiya anati: Kodi ndikuona chiyani?

Achita mantha

akubwerera,

ankhondo awo agonjetsedwa.

Akuthawa mofulumirapo

osayangʼananso mʼmbuyo,

ndipo agwidwa ndi mantha ponseponse,”

akutero Yehova.

6Waliwiro sangathe kuthawa

ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kupulumuka.

Akunka napunthwa ndi kugwa

kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.

7“Kodi ndani amene akukwera ngati Nailo,

ngati mtsinje wa madzi amkokomo?

8Igupto akusefukira ngati Nailo,

ngati mitsinje ya madzi amkokomo.

Iye akunena kuti, ‘Ndidzadzuka ndi kuphimba dziko lapansi;

ndidzawononga mizinda ndi anthu ake.’

9Tiyeni, inu akavalo!

Thamangani inu magaleta!

Tulukani, inu ankhondo,

ankhondo a ku Kusi ndi Puti amene mumanyamula zishango,

ankhondo a ku Ludi amene mumaponya uta.

10Koma tsikulo ndi la Ambuye Yehova Wamphamvuzonse;

tsiku lolipsira, lolipsira adani ake.

Lupanga lake lidzawononga ndi kukhuta magazi,

lidzaledzera ndi magazi.

Pakuti Yehova, Yehova Wamphamvuzonse, adzapereka adani ake ngati nsembe

mʼdziko la kumpoto mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.

11“Pita ku Giliyadi ukatenge mankhwala

iwe namwali Igupto.

Wayesayesa mankhwala ambiri koma osachira;

palibe mankhwala okuchiritsa.

12Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako;

kulira kwako kwadzaza dziko lapansi.

Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana,

onse awiri agwa pansi limodzi.”

13Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za kubwera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kudzathira nkhondo Igupto ndi uwu:

14“Mulengeze ku Igupto. Mulengeze ku Migidoli.

Mulengezenso ku Mefisi ndi ku Tapanesi.

Muwawuze anthu akumeneko kuti, ‘Imani pamalo panu ndi kukhala okonzeka kudziteteza,

chifukwa lupanga lidzawononga zonse zimene muli nazo.’

15Chifukwa chiyani mulungu wanu wamphamvu uja Apisi wathawa?

Iye sakanatha kulimba chifukwa Yehova anamugwetsa.

16Ankhondo anu apunthwa ndi kugwa.

Aliyense akuwuza mnzake kuti,

‘Tiyeni tibwerere kwathu,

ku dziko kumene tinabadwira,

tithawe lupanga la adani athu.’

17Kumeneku iwo adzafuwula kuti,

‘Farao, mfumu ya ku Igupto mupatseni dzina lakuti,

Waphokoso, Wotaya mwayi wake.’

18“Pali Ine wamoyo,” ikutero Mfumu,

imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse,

“wina adzabwera amene ali ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena,

ngati phiri la Karimeli loti njoo mʼmbali mwa nyanja.

19Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo

inu anthu a ku Igupto,

pakuti Mefisi adzasanduka chipululu

ndipo adzakhala bwinja mopanda wokhalamo.

20“Igupto ali ngati mwana wangʼombe wokongola,

koma chimphanga chikubwera

kuchokera kumpoto kudzalimbana naye.

21Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye

ali ngati ana angʼombe onenepa.

Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi.

Palibe amene wachirimika.

Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira;

ndiyo nthawi yowalanga.

22Aigupto akuthawa ndi liwu lawo lili ngati la njoka yothawa

pamene adani abwera ndi zida zawo,

abwera ndi nkhwangwa

ngati anthu odula mitengo.

23Iwo adzadula nkhalango ya Igupto,”

akutero Yehova,

“ngakhale kuti ndi yowirira.

Anthuwo ndi ochuluka kupambana dzombe,

moti sangatheke kuwerengeka.

24Anthu a ku Igupto achita manyazi

atengedwa ukapolo ndi anthu a kumpoto.”

25Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira. 26Ndidzawapereka kwa amene akufuna kuwapha, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi atsogoleri ake ankhondo. Komabe, mʼtsogolomo Igupto adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Yehova.

27“Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha;

usataye mtima, iwe Israeli.

Ndithu Ine ndidzakupulumutsa kuchokera ku mayiko akutali,

ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera ku mayiko kumene anapita nazo ku ukapolo.

Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala motakasuka ndi pa mtendere,

ndipo palibenso wina amene adzamuopsa.

28Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha,

pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova.

“Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu

a ku mayiko kumene ndakupirikitsira,

Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu.

Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera;

sindidzakulekerera osakulanga.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 46:1-28

关于埃及的预言

1耶和华把有关列国的事告诉了耶利米先知。 2犹大约西亚的儿子约雅敬执政第四年,埃及王法老尼哥的军队在幼发拉底河边的迦基米施巴比伦尼布甲尼撒击败。论到埃及,耶和华说:

3“要预备大小盾牌,

冲向战场。

4要套好战车,

骑上战马,

擦亮矛枪,

顶盔贯甲。

5可是,我看见的是什么呢?

他们惊慌后退,

勇士败逃,不敢回头,

惊恐不安。

这是耶和华说的。

6善跑者跑不掉,

强壮者逃不了,

他们扑倒在北面的幼发拉底河边。

7“那如尼罗河涨溢,

如江水奔腾的是谁呢?

8埃及尼罗河涨溢,

如江水奔腾。

她说,‘我要涨溢,淹没大地,

毁灭城邑和其中的居民。’

9战马奔驰吧!

战车疾驶吧!

勇士啊,就是那些手拿盾牌的古实人和人以及箭法娴熟的吕底亚人啊,出战吧!

10因为这是主——万军之耶和华向敌人报仇的日子。

刀剑必吞噬他们,

痛饮他们的血,

因为要在北方的幼发拉底河边向主——万军之耶和华献祭。

11埃及人啊,

基列取乳香吧!

然而,再多的良药也无法医治你们。

12你们的耻辱传遍列国,

你们的哀哭响彻大地,

你们的勇士彼此碰撞,

倒在一起。”

13论到巴比伦尼布甲尼撒要来攻打埃及的事,耶和华对耶利米先知说:

14“你要在埃及宣布,在密夺挪弗答比匿宣告,

‘你们要准备战斗,

因为刀剑要吞噬你们周围的人。’

15你们的勇士为何扑倒?

他们无法坚立,

因为耶和华击倒了他们,

16使他们跌跌绊绊,纷纷倒下。

他们说,‘起来,我们回到同胞那里,回到故乡吧,

好躲避敌人的刀剑。’

17他们在那里喊叫,

埃及王法老只会虚张声势,

他已错失良机。’”

18名叫万军之耶和华的王说:

“我凭我的永恒起誓,

将有一位要来,

他的气势如群山中的他泊山,

又像海边的迦密山。

19住在埃及的子民啊,

收拾行装准备流亡吧!

因为挪弗必被烧毁,

沦为废墟,杳无人迹。

20埃及像头肥美的母牛犊,

但从北方却来了牛虻。

21埃及的佣兵好像肥牛犊,

都转身逃之夭夭,无力抵挡,

因为他们遭难、受罚的日子到了。

22“敌军进攻的时候,

埃及必像蛇一样嘶嘶地溜走。

敌军必拿着斧头蜂拥而来,

像樵夫砍树一样攻击他们。

23埃及的人口虽然稠密如林,

敌军必像无数的蝗虫一样扫平他们。

这是耶和华说的。

24埃及人必蒙羞,

落在北方人的手中。”

25以色列的上帝——万军之耶和华说:“看啊,我要惩罚提比斯的神明亚扪埃及的其他神明、法老、首领以及依靠法老的人。 26我要把他们交在想杀他们的巴比伦尼布甲尼撒及其官长手中。然而,日后埃及必再有人居住,如往日一样。这是耶和华说的。

27“我的仆人雅各啊,不要害怕!

以色列人啊,不要惊慌!

因为我要从远方把你们救回来,

使你们从流亡之地归回。

你们必重返家园,安享太平,

无人搅扰。

28我的仆人雅各啊,不要害怕,

因为我与你同在。

我曾使你流亡到列国,

我必彻底毁灭列国,

但不会彻底毁灭你,

也不会饶过你,

我必公正地惩治你。

这是耶和华说的。”