Yeremiya 43 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 43:1-13

1Yeremiya atatsiriza kuwawuza anthuwo mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova anamutuma kuti akawawuze, 2Azariya mwana wa Hosayia ndi Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi anthu onse odzikuza anawuza Yeremiya kuti, “Ukunama iwe! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti unene kuti, ‘Musapite ku Igupto kukakhala kumeneko.’ 3Koma ndi Baruki mwana wa Neriya amene akukulimbikitsa kuti utiletse zopita ku Igupto ndi kuti mʼmalo mwake tidzipereke mʼmanja mwa Ababuloni, kuti iwo atiphe kapena kutitenga ukapolo ku Babuloni.”

4Motero Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi anthu onse sanamvere lamulo la Yehova loti akhale mʼdziko la Yuda. 5Mʼmalo mwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo anatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene anabwera kudzakhala mʼdziko la Yuda kuchokera ku mayiko onse kumene anabalakirako. 6Mʼgulu la anthu otengedwalo munali amuna onse, akazi ndi ana, ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anawasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani pamodzinso ndi mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya. 7Kotero anthuwo analowa mʼdziko la Igupto chifukwa anakana kumvera Yehova, nakafika ku Tapanesi.

8Ndipo Yehova anayankhula ndi Yeremiya ku Tapanesi kuti, 9“Tenga miyala inayi yayikulu ndipo uyikwirire mʼdothi pa chiwundo cha polowera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Uchite zimenezi Ayuda onse akuona. 10Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayitana mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzakhazika mpando wake waufumu pa miyala imene ndayikwirira apayi. Iye adzafunyulula tenti yake yaufumu pa miyala imeneyi. 11Iye adzabwera kudzathira nkhondo Igupto. Iwo oyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri, iwo oyenera kutengedwa ukapolo adzatengedwa ukapolo, ndipo iwo oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga. 12Adzayatsa moto mʼnyumba zopembedzera milungu ya Igupto. Adzayeretsa dziko la Igupto monga momwe mʼbusa amayeretsera chovala chake pochotsamo nsabwe. Pambuyo pake adzachoka mʼdziko la Igupto mwa mtendere. 13Ku Iguptoko adzagwetsa zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzera mulungu wa dzuwa. Adzatentha ndi moto nyumba za milungu ya ku Igupto.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 43:1-13

耶利米被带到埃及

1耶利米向众人宣告了他们的上帝耶和华的话,就是他们的上帝耶和华派他去说的一切话。 2何沙雅的儿子亚撒利雅加利亚的儿子约哈难和一些狂妄之徒对耶利米说:“你在撒谎!我们的上帝耶和华并没有派你来告诉我们不可去埃及住。 3尼利亚的儿子巴录怂恿你反对我们,好叫我们落在迦勒底人手中,任由他们宰杀或掳到巴比伦。” 4于是,加利亚的儿子约哈难和众将领及民众都不听从耶和华让他们留在犹大的命令。 5-7加利亚的儿子约哈难和众将领率领民众下到埃及答比匿。民众中有流亡到各国又返回犹大的余民和护卫长尼布撒拉旦留给沙番的孙子、亚希甘的儿子基大利管理的男女妇孺、公主以及耶利米先知和尼利亚的儿子巴录。他们没有听从耶和华的命令。

8耶和华在答比匿耶利米说: 9“你当着犹大人的面搬几块大石头,埋在答比匿的法老宫门前的砖路下面, 10然后告诉他们以色列的上帝——万军之耶和华说,‘看啊,我必召来我的仆人巴比伦尼布甲尼撒,把他的宝座安置在我让你埋的石头上面,他要在上面搭起他的帐篷。 11他要前来攻打埃及,叫那些该死的死、该被掳的被掳、该被杀的被杀。 12他要焚烧埃及的神庙,掳走神像;他要像牧人披上外衣一样轻而易举地征服埃及,然后安然离去。 13他要摧毁埃及太阳神庙的神柱,烧毁埃及的神庙。’”