Yeremiya 4 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 4:1-31

1“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,

bwererani kwa Ine,”

akutero Yehova.

“Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga

ndipo musasocherenso.

2Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo

kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’

Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse

ndipo adzanditamanda.”

3Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:

“Limani masala anu

musadzale pakati pa minga.

4Dziperekeni nokha kwa Ine

kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,

inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.

Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,

chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo

popanda wina wowuzimitsa.

Adani Ochokera Kumpoto kwa Yuda

5“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,

‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’

Ndipo fuwulani kuti,

‘Sonkhanani!

Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’

6Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!

Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!

Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,

kudzakhala chiwonongeko choopsa.”

7Monga mkango umatulukira mʼngaka yake

momwemonso wowononga mayiko

wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.

Watero kuti awononge dziko lanu.

Mizinda yanu idzakhala mabwinja

popanda wokhalamo.

8Choncho valani ziguduli,

lirani ndi kubuwula,

pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova

sunatichokere.

9“Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,

ansembe adzachita mantha kwambiri,

ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”

akutero Yehova.

10Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”

11Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; 12koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”

13Taonani, adani akubwera ngati mitambo,

magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu,

akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga.

Tsoka ilo! Tawonongeka!

14Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.

Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?

15Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;

akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.

16Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,

lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,

‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,

akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.

17Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda,

chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ”

akutero Yehova.

18“Makhalidwe anu ndi zochita zanu

zakubweretserani zimenezi.

Chimenechi ndiye chilango chanu.

Nʼchowawa kwambiri!

Nʼcholasa mpaka mu mtima!”

19Mayo, mayo,

ndikumva kupweteka!

Aa, mtima wanga ukupweteka,

ukugunda kuti thi, thi, thi.

Sindingathe kukhala chete.

Pakuti ndamva kulira kwa lipenga;

ndamva mfuwu wankhondo.

20Tsoka limatsata tsoka linzake;

dziko lonse lasanduka bwinja.

Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa,

mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.

21Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,

ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?

22Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;

iwo sandidziwa.

Iwo ndi ana opanda nzeru;

samvetsa chilichonse.

Ali ndi luso lochita zoyipa,

koma sadziwa kuchita zabwino.”

23Ndinayangʼana dziko lapansi,

ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;

ndinayangʼana thambo,

koma linalibe kuwala kulikonse.

24Ndinayangʼana mapiri,

ndipo ankagwedezeka;

magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.

25Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;

mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.

26Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;

mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja

pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.

27Yehova akuti,

“Dziko lonse lidzasanduka chipululu

komabe sindidzaliwononga kotheratu.

28Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira

ndipo thambo lidzachita mdima,

pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,

ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”

29Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,

anthu a mʼmizinda adzathawa.

Ena adzabisala ku nkhalango;

ena adzakwera mʼmatanthwe

mizinda yonse nʼkuyisiya;

popanda munthu wokhalamo.

30Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja!

Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira

ndi kuvalanso zokometsera zagolide?

Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera,

ukungodzivuta chabe.

Zibwenzi zako zikukunyoza;

zikufuna kuchotsa moyo wako.

31Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,

kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.

Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.

Atambalitsa manja awo nʼkumati,

“Kalanga ife! Tikukomoka.

Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”

King James Version

Jeremiah 4:1-31

1If thou wilt return, O Israel, saith the LORD, return unto me: and if thou wilt put away thine abominations out of my sight, then shalt thou not remove. 2And thou shalt swear, The LORD liveth, in truth, in judgment, and in righteousness; and the nations shall bless themselves in him, and in him shall they glory.

3¶ For thus saith the LORD to the men of Judah and Jerusalem, Break up your fallow ground, and sow not among thorns. 4Circumcise yourselves to the LORD, and take away the foreskins of your heart, ye men of Judah and inhabitants of Jerusalem: lest my fury come forth like fire, and burn that none can quench it, because of the evil of your doings.

5Declare ye in Judah, and publish in Jerusalem; and say, Blow ye the trumpet in the land: cry, gather together, and say, Assemble yourselves, and let us go into the defenced cities. 6Set up the standard toward Zion: retire, stay not: for I will bring evil from the north, and a great destruction.4.6 retire: or, strengthen4.6 destruction: Heb. breaking 7The lion is come up from his thicket, and the destroyer of the Gentiles is on his way; he is gone forth from his place to make thy land desolate; and thy cities shall be laid waste, without an inhabitant. 8For this gird you with sackcloth, lament and howl: for the fierce anger of the LORD is not turned back from us. 9And it shall come to pass at that day, saith the LORD, that the heart of the king shall perish, and the heart of the princes; and the priests shall be astonished, and the prophets shall wonder. 10Then said I, Ah, Lord GOD! surely thou hast greatly deceived this people and Jerusalem, saying, Ye shall have peace; whereas the sword reacheth unto the soul. 11At that time shall it be said to this people and to Jerusalem, A dry wind of the high places in the wilderness toward the daughter of my people, not to fan, nor to cleanse, 12Even a full wind from those places shall come unto me: now also will I give sentence against them.4.12 a full…: or, a fuller wind than those4.12 give…: Heb. utter judgments 13Behold, he shall come up as clouds, and his chariots shall be as a whirlwind: his horses are swifter than eagles. Woe unto us! for we are spoiled. 14O Jerusalem, wash thine heart from wickedness, that thou mayest be saved. How long shall thy vain thoughts lodge within thee? 15For a voice declareth from Dan, and publisheth affliction from mount Ephraim. 16Make ye mention to the nations; behold, publish against Jerusalem, that watchers come from a far country, and give out their voice against the cities of Judah. 17As keepers of a field, are they against her round about; because she hath been rebellious against me, saith the LORD. 18Thy way and thy doings have procured these things unto thee; this is thy wickedness, because it is bitter, because it reacheth unto thine heart.

19¶ My bowels, my bowels! I am pained at my very heart; my heart maketh a noise in me; I cannot hold my peace, because thou hast heard, O my soul, the sound of the trumpet, the alarm of war.4.19 my very…: Heb. the walls of my heart 20Destruction upon destruction is cried; for the whole land is spoiled: suddenly are my tents spoiled, and my curtains in a moment. 21How long shall I see the standard, and hear the sound of the trumpet? 22For my people is foolish, they have not known me; they are sottish children, and they have none understanding: they are wise to do evil, but to do good they have no knowledge. 23I beheld the earth, and, lo, it was without form, and void; and the heavens, and they had no light. 24I beheld the mountains, and, lo, they trembled, and all the hills moved lightly. 25I beheld, and, lo, there was no man, and all the birds of the heavens were fled. 26I beheld, and, lo, the fruitful place was a wilderness, and all the cities thereof were broken down at the presence of the LORD, and by his fierce anger. 27For thus hath the LORD said, The whole land shall be desolate; yet will I not make a full end. 28For this shall the earth mourn, and the heavens above be black: because I have spoken it, I have purposed it, and will not repent, neither will I turn back from it. 29The whole city shall flee for the noise of the horsemen and bowmen; they shall go into thickets, and climb up upon the rocks: every city shall be forsaken, and not a man dwell therein. 30And when thou art spoiled, what wilt thou do? Though thou clothest thyself with crimson, though thou deckest thee with ornaments of gold, though thou rentest thy face with painting, in vain shalt thou make thyself fair; thy lovers will despise thee, they will seek thy life.4.30 face: Heb. eyes 31For I have heard a voice as of a woman in travail, and the anguish as of her that bringeth forth her first child, the voice of the daughter of Zion, that bewaileth herself, that spreadeth her hands, saying, Woe is me now! for my soul is wearied because of murderers.